الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Ndithudi Ife takupambanitsa iwe,kupambana kwenikweni
25.Iwo ndiwo amene sadakhulupirire ndipo adakutchingani kuti musalowe mu Mzikiti Wolemekezeka ndi kukuletsani kuti nyama za nsembe zisakafike pa malo operekerapo nsembe. Koma pakadakhala kuti panalibe anthu aamuna okhulupirira ndi aakazi okhulupirira, amene simuwadziwa, inu mukadawapondereza kotero kuti china chake choipa chikadadza pa inu chifukwa cha iwo, kuti Mulungu aonetse chisomo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma iwo akadapatukana wina ndi mnzake, Ife ndithudi tikadalanga ndi chilango choopsa onse amene sadakhulupirire amene anali pakati pawo
29.Muhammad ndi Mtumwi wa Mulungu ndipo onse amene amamutsatira iye amakhala olimbika polimbana ndi anthu osakhulupirira koma amachitirana chisoni wokhaokha. Inu mumawaona ali nkupembedza pa mawondo awo ndi kugwetsa mphumi zawo kufunafuna chisomo chochokera kwa Mulungu ndi chisangalalo chake. Pamphumi pawo pali zizindikiro zimene zimadza chifukwa chakugunditsa mphumi zawo pansi. Awa ndi maonekedwe awo amene ali m’Chipangano Chakale. Koma maonekedwe awo amene ali mu Chipangano Chatsopano ali monga momwembewuimatulutsiransongayakendikuikhwimitsa. Ndipo iyo imalimba ndi kukhala yoimirira modabwitsa ndi kusangalatsa amene adaibzala. Kuti Iye akwiyitse osakhulupirira ndi izo. Mulungu walonjeza chikhululukiro ndi mphotho yaikulu kwa anthu okhulupirira ndiponso ochita ntchito zabwino