الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Iwo amene sakhulupirira ndipo amaletsa anzawo kutsatira njira ya Mulungu, Iye adzasandutsa ntchito zawo kukhala zopanda pake
4.Motero pamene inu mukumana ndi anthu osakhulupirira pa nkhondo, thyolani makosi awo, mpaka pamene mukupha ndi kuvulaza ambiri ndipo muwagwire kukhala akaidi ndipo pambuyo pake mukhoza kuwamasula powaonetsa chisoni kapena akhale ngati chigwiriro mpaka pamene nkhondo itatha. Motero inu mwalamulidwa. Koma chikadakhala chifuniro cha Mulungu, ndithudi, Iye Mwini wake akadawapatsa chilango chowayenera. Koma Iye wafuna kuti inu mumenyane nawo ndi cholinga chokuyesani wina ndi mnzake. Koma iwo amene aphedwa m’njira ya Mulungu, Iye sadzalola kuti ntchito zawo zipite pachabe