الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Oh inu anthu okhulupirira! Musadzikweze pamaso pa Mulungu ndi pa Mthenga wake, koma opani Mulungu chifukwa Iye ndiye amene amamva ndi kudziwa chinthu china chilichonse
11.oh inu anthu okhulupirira! Musalole kuti anthu ena aziseka anzawo. Mwina kungatheke kuti gulu limene lisekedwa likhoza kukhala labwino kuposa limene likuseka. Ndiponso musalole akazi kuti aseke anzawo chifukwa mwina kungatheke kuti osekedwawo akhoza kukhala abwino kuposa osekawo. Musafunirane zifukwa wina ndi mnzake kapena kuitanana ndi mayina a mchedzera. Mayina a mchedzera ndi oipa kwa amene wakhulupirira. Ndipo aliyense amene sasiya kuitana anzake ndi maina a mchedzera , ameneyo ndiye wopanda chilungamo