1.Oh iwe Mtumwi! Opa Mulungu ndipo usamvere zonena za anthu osakhulupirira ndi a chinyengo. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha
2.Koma tsatira zonse zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako ndithudi Mulungu amadziwa zimene umachita
4.Mulungusadalengemitimaiwirim’chifuwachamunthu, ndipo Iye sadalenge akazi anu amene mumawasudzula chifukwa chakuti amalingana ndi amayi anu, ndipo sadawalenge ana omwe mkazi wanu adabereka ndi mwamuna wina kukhala ana anu enieni. Zimenezo ndizo zongokamba zanu chabe koma Mulungu ali kukuuzani inu choonadi ndipo Iye amalangiza njira yoyenera
5.Aitaneni ndi mayina atate awo ana onse omwe mkazi wanu adaberaka ndi mwamuna wina chifukwa chimenecho ndicho chilungamo pamaso pa Mulungu. Koma ngati inu simudziwa mayina atate awo, pamenepo iwo ndi abale anu m’chipembedzo kapena abwenzi. Koma palibe cholakwa kwa inu ngati mulakwitsa. Chimene chifunika kwenikweni ndi cholinga chimene chili mu mtima mwanu. Ndithudi Mulungu amakhululukira nthawi zonse ndipo ndi mwini chisoni chosatha
6.Mtumwi ali ndi udindo waukulu pa anthu okhulupirira kuposa umene iwo ali nawo pakati pa wina ndi mnzake ndipo akazi a Mtumwi ali ngati amayi awo. Ndipo ubale wa magazi amodzi pakati pawo umawabweretsa pafupi wina ndi mnzake. M’Buku la Mulungu, ubale umene umadza kwa iwo amene akhulupirira uposa amene amathawa ku nyumba kwawo. Ngakhale zili choncho inu muyenera kuonetsa zabwino kwa abwenzi anu. Zimenezi ndizo zimene zidalembedwa m’Buku la Mulungu
7.Kumbukira pamene tidalandira lonjezo lochokera kwa Atumwi ndi kwa iwe. Ndiponso kuchokera kwa Nowa, Abrahamu, Mose, ndi Yesu mwana wamwamuna wa Maria. Tidalandira lonjezo lokhazikika kuchokera kwa iwo
8.Kuti Mulungu akhoza kufunsa anthu olungama za chilungamo chawo ndipo Iye wawakonzera anthu osakhulupirira chilango chowawa kwambiri
9.oh inu anthu okhulupirira! Kumbukirani chisomo cha Mulungu pa inu pamene kudadza gulu la adani. Koma Ife tidatumiza, kuti iwagonjetse, mphepo ya mkuntho ndi Asirikali amene inu simudawaone. Koma Mulungu amaona zonse zimene mumachita
10.Pamene iwo adadza kwa inu kuchokera kumwamba ndi kuchokera padziko lapansi ndiponso pamene maso adatembenuka, mitima yanu idafumuka mpaka pakhosi ndipo inu mudayamba kuganiza maganizo oipa okhudza Mulungu
12.Ndipo taona! Anthu onse a chinyengo ndi iwo amene mu mitima mwawo muli matenda adati, “Mulungu pamodzi ndi Mtumwi wake sadatilonjeze china chilichonse koma chinyengo.”
13.Taona! Gulu lina limene lidali pakati pawo lidati, “Inu anthu a ku Yasrib simungawagonjetse awa ayi kotero bwererani m’mbuyo!” Ndipo kagulu kena kamapempha chilolezo kwa Mtumwi ndipo kadati, “Ndithudi nyumba zathu zilibe woziteteza.” Koma sizinali choncho ayi koma kuti iwo amangofuna kupeza njira yothawira
14.Ndipo mdani akadalowa kudzera pachipata cha mbali ina ya mzindawu, ndipo iwo akadafunsidwa kuti aleke chisilamu. Ndithudi, iwo akadachita chomwecho. Ndipo sakadakayika kutero, ngakhale mpang’ono pomwe
15.Komatu iwo adalonjeza kale kwa Mulungu kuti sadzabwerera m’mbuyo ndipo lonjezo la Mulungu liyenera kukwaniritsidwa
16.Nena, “Kuthawa sikudzakuthandizani inu ngati inu muli kuthawa imfa, kapena kuphedwa. Ndipo ngakhale kuti inu mungathawe, mudzangosangalala m’moyo wa pa dziko lino lapansi pa kanthawi kochepa chabe.”
17.Nena, “Kodi ndani amene angakutetezeni inu kwa Mulungu ngati iye atafuna kuti akulangeni inu? Kodi ndani amene akhoza kumuletsa Mulungu ngati atafuna kuti akuonetseni chifundo chake?” Ndipo iwo sadzapeza wina kupatula Mulungu kukhala mtetezi kapena mthandizi wawo
18.Ndithudi Mulungu amawadziwa onse amene amaletsa anzawo ndi iwo amene amauza abale awo kuti, “Bwerani kwa ife.” Pamene iwo sadza ku nkhondo kupatula ochepa
19.Ndi njiru imene ali nayo pa iwe, pamene choopsa chidza, iwe udzawaona ali kukuyang’ana, maso awo ali kutembenuzika, monga munthu amene ali pafupi kufa. Komangatichoopsachidutsaiwoamakunyozandimalirime awo akuthwa chifukwa cha njiru pa zinthu zabwino zimene uli nazo. Awa sadakhulupirire ndipo Mulungu wasandutsa zochita zawo kukhala zopanda pake ndipo zimenezi si zovuta kwa Mulungu
20.Iwo akuganiza kuti owathandiza awo alipo ndipo ngati iwo akadabweranso iwo akadafuna akadakhala ali m’chipululu pamodzi ndi anthu okhala m’chipululu ndi kufunsa nkhani zokhudza iwe kuchokera kutali. Ndipo iwo akadakhala pakati panu, akadamenya nkhondo pang’ono
21.Ndithudi muli chitsanzo chabwino mwa Mtumwi wa Mulungu kwa iye amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ndipo amakumbukira Mulungu kwambiri
22.Pamene anthu okhulupirira adaona anzawo owathandiza, iwo adati, “Ichi ndi chimene Mulungu ndi Mtumwi wake adatilonjeza. Ndithudi Mulungu ndi Mtumwi wake adatiuza zoona.” Ndipo izi zidaonjezera chikhulupiriro chawo ndi kudzipereka kwawo kwathunthu
23.Pakati pa okhulupirira pali anthu amene amakwaniritsa lonjezo limene adachita ndi Mulungu. Ena mwa iwo adafa ndipo ena akadadikira. Koma iwo sadasinthe maganizo ngakhale pang’ono
24.Kuti Mulungu akhoza kupereka malipiro kwa anthu olungama chifukwa cha chilungamo chawo ndi kulanga anthu a chinyengo ngati chimenecho ndicho chifuniro chake kapena kuwakhululukira chifukwa Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
25.Ndipo Mulungu adawabweza anthu osakhulupirira atakwiya. Iwo sadapeze chabwino china chilichonse ndipo Mulungu adawathandiza anthu okhulupirira pomenya nkhondo. Ndipo Mulungu ndi wamphamvu zambiri
26.Ndipo anthu a m’Buku amene adawathandiza iwo, Mulungu adawachotsa kumalo awo okhazikika ndipo adakhazika mantha m’mitima mwawo, kotero inu mudapha ena ndi ena mudawagwira ukapolo
27.Ndipo Iye adakupatsani dziko lawo, nyumba zawo, ndi katundu wawo ndi dziko limene inu simuyendamo. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
28.Oh iwe Mtumwi! Auze akazi ako kuti, “Ngati inu mukonda moyo wa dziko lino ndiponso zosangalatsa zake, bwerani, ine ndidzakupatsani zosangalatsa zake ndipo ndidzakulolani kuti muchoke bwinobwino.”
29.Ndipo ngati inu mufuna Mulungu ndi Mtumwi wake ndi moyo umene uli nkudza, ndithudi, Mulungu wawakonzera mphotho yaikulu anthu ochita zabwino amene ali pakati panu
30.oh inu akazi a Mtumwi! Aliyense wa inu amene achita choipa poyera, chilango chake chidzaonjezedwa kawiri ndipo kutero ndi kwapafupi kwa Mulungu
31.Ndipo aliyense wa inu amene ndi omvera Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amachita ntchito zabwino, Ife tidzamupatsa malipiro ake kawiri ndipo tamukonzera iye chakudya cholemekezeka
32.Oh inu akazi a Mtumwi! Inu simuli akazi wamba. Ngati inu mumaopa Mulungu, muziwayankhula mawu okoma chifukwa mwina anthu amene mu mtima mwawo muli matenda akhoza kuyamba kukusirirani. Koma yankhulani mawu abwino
33.Ndipo khalani mwakachetechete m’nyumba zanu ndipo musachite zinthu zoipa zoti muonekere poyera monga mmene amachitira anthu nthawi yaumbuli. Ndipo pitirizani kupemphera, perekani msonkho wothandiza anthu osauka ndipo muzimvera Mulungu ndi Mtumwi wake yemwe. Ndipo Mulungu angofuna kuchotsa uve umene uli mwa inu anthu a pabanja lake, ndikukuyeretsani inu
34.Ndipo kumbukirani chimene chaphunzitsidwa kwa inu m’nyumba mwanu cha zizindikiro za Mulungu ndi luntha lake. Chifukwa Mulungu ndiye mwini chifundo ndipo amadziwa chilichonse
35.Ndithudi a Chisilamu amene amakhulupirira ndi amuna ndi akazi okhulupirira, amuna ndi akazi a chilungamo, amuna ndi akazi opirira, amuna ndi akazi ofatsa, amuna ndi akazi othandiza osauka, amuna ndi akazi osala, ndi amuna ndi akazi osachita chiwerewere ndi amuna ndi akazi amene amakumbukira Mulungu kwambiri; kwa anthu onse otere, Mulungu wawakonzera chikhululukiro ndi mphotho yaikulu
36.Si koyenera kwa munthu wokhulupirira wamwamuna kapena wamkazi kuti pamene nkhani yalamulidwa ndi Mulungu ndi Mtumwi wake, kuti anene china chilichonse pa chiweruzo cha nkhaniyo. Ngati wina samvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, iye ali wosochera moonekeratu
37.Ndi pamene iwe udamuuza wina amene adalandira chisomo cha Mulungu ndi chifundo chake kuti, “Musunge mkazi wako ndipo uope Mulungu.” Ndipo iwe udabisa mu mtima mwako zimene Mulungu akadaulula ndipo iwe udaopaanthupamenekunalikoyenerakutiuziopaMulungu. Ndipo pamene Zaid adamusudzula iye, tidamukwatitsa iye kwa iwe ndi cholinga chakuti kutsogolo kusadzakhale vuto kwa anthu okhulupirira pa nkhani ya ukwati wokhudzana ndi ana owapeza pamene iwo asudzulana. Ulamuliro wa Mulungu uyenera kukwaniritsidwa
38.Palibe vuto kwa Mtumwi pa zimene Mulungu wamupatsa ngati udindo wake. Chidali chizolowezi cha Mulungu kwa anthu amene adalipo kale. Ndipo ulamuliro wa Mulungu ndi wokhazikika
39.Iwo amene amalalikira uthenga wa Mulungu ndipo amene amamuopa Iye, iwo saopa wina aliyense koma Mulungu ndipo Mulungu ndi wokwanira kubwezera
40.Muhammad si atate wa wina aliyense wa inu koma iye ndi Mthenga wa Mulungu ndi womaliza wa Atumwi a Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
43.Ndiye amene amapereka madalitso ake pa inu ndipo angelo ake amachita chimodzimodzi kuti Iye akhoza kukuchotsani inu ku mdima kupita kowala. Ndipo Iye ndi wachifundo kwa okhulupirira
44.Kulonjerana kwawo pa tsiku limene adzakumana naye kudzakhala adzati,“Mtendere”. Ndipo Iye wawakonzera mphotho yolemekezeka
47.Kotero auze nkhani yabwino anthu okhulupirira kuti adzalandira mphatso yaikulu kuchokera kwa Mulungu
48.Ndipo usamvere zilakolako za anthu osakhulupirira ndi za anthu a chinyengo. Usalabadire zonena zawo koma ika chikhulupiriro chako mwa Mulungu. Mulungu ndi wokwana kukhala Mtetezi
49.Oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukwatira akazi okhulupirira ndipo muwasudzula musanalowane nawo, palibe nthawi yoyembekezera pakhomo panu. Kotero asanachoke apatseni mphatso yawo ndipo alekeni kuti achoke mwaubwino
50.Oh iwe Mtumwi! Takulola kukhala ndi akazi onse amene iwe wapereka chiongo chawo ndi iwo amene ndi akapolo ako kuchokera kugulu limene lidagwidwa pankhondo ndipo Mulungu wakupatsa iwe; ana a akazi a atsibweni ndi azakhali ako, a kuchimuna kapena kuchikazi amene adachoka pamodzi ndi iwe. Ndiponso mkazi wina aliyense wokhulupirira amene adzipereka yekha kwa Mtumwi ngati Mtumwi afuna kumukwatira iye. Chilolezo ichi ndi cha iwe wekha osati cha anthu onse okhulupirira. Ife tikudziwa chimene tawasankhira iwo zokhudza akazi awo ndi akapolo amene iwo amasunga, ndi cholinga chakuti pasadzakhale vuto kwa iwe. Ndipo Mulungu amakhululukira nthawi zonse ndipo ndiye Mwini chisoni chosatha
51.Iwe ukhoza kumusiya aliyense wa iwo amene wafuna ndipo ukhoza kutenga aliyense wa iwo amene wafuna ndi aliyense wa iwo amene udawasiya pa kanthawi kochepa. Palibe cholakwa kwa iwe pochita izi kuti maso awo azizire ndiponso onse asadandaule ndi zimene uwapatsa. Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zomwe zili m’mitima mwanu. Mulungu amadziwa zonse ndiponso ndi wopirira
52.Iwe siuloledwa kukwatiranso akazi ena pambuyo pa awa kapena kuwasintha kuti upeze akazi ena ngakhale kuti kukongola kwawo kuli kukusangalatsa kupatula akapolo amene uli nawo. Ndipo Mulungu amayang’anitsitsa pa zinthu zonse
53.Oh inu anthu okhulupirira! Musamalowe m’nyumba za Mtumwi pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kuti mukadye chakudya osati kukadikira chakudya mpaka pamene chiphikidwa. Koma pamene mwaitanidwa lowani ndipo pamene mumaliza kudya chokani. Musayembekeze kumvetsera nkhani. Ndithudi zimenezi zimamupatsa Mtumwi mavuto koma iye amachita nanu manyazi pamene Mulungu sachita manyazi kuulula choonadi. Ndipo ngati inu mufunsa katundu wina aliyense, funsani kuchokera ku malo osaonekera. Ichi ndi chabwino kwa inu ndiponso kwa iwo ndipo si koyenera kuti inu mumupatse mavuto Mtumwi wa Mulungu kapena kuti inu mukwatire akazi ake iye atawasiya. Ndithudi chimenechi ndi chinthu choipa pamaso pa Mulungu
54.Ngati inu muchita chinthu poyera kapena mobisa, ndithudi, dziwani kuti Mulungu amadziwa zinthu zonse
55.Palibe cholakwa kwa iwo pa nkhani zokhudza atate awo kapena ana awo kapena abale awo kapena ana a abale awo kapena akazi awo kapena atumiki awo. Ndipo opani Mulungu. Ndithudi, Mulungu ndi mboni pa chinthu china chilichonse
56.Ndithudi Mulungu ndi angelo amamudalitsa Mtumwi wake. oh inu anthu okhulupirira! Pemphani madalitso kuti adze pa iye ndipo mulonjereni ndi malonje abwino
57.Ndithudi iwo amene amanena zinthu zoipa zokhudza Mulungu ndi Mtumwi wake, Mulungu anawatemberera iwo m’moyo uno ndiponso adzawatemberera m’moyo umene uli nkudza ndipo wawakonzera chilango chochititsa manyazi
58.Ndipo iwo amene amayankhula zinthu zoipa zokhudza anthu a amuna okhulupirira ndi anthu a akazi okhulupirira, pamene iwo sadalakwe, iwowo ali pamlandu wonamizira ndi wochita tchimo looneka
59.Oh iwe Mtumwi! Auze akazi ako ndi ana ako, akazi ndi akazi a anthu okhulupirira kuti azivala moyenera zovala zawo zapamwamba zoonjezera pa zovala zomwe avala mkati. Zimenezi zidzakhala zabwino kuti akhoza kudziwika nazo ndipo kotero iwo sadzavutitsidwa ayi. Ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
60.Ngati anthu achinyengo pamodzi ndi iwo amene m’mitima mwawo muli matenda ndiponso anthu amene amayambitsa chisokonezo mu mzinda, saleka mchitidwe oterewu,** ndithudi, Ife tidzalimbana nawo ndipo iwo sadzakhala pafupi ndi inu kupatula nthawi yochepa
62.Amenewa ndiwo adali machitidwe a Mulungu kwa anthu akale ndipo inu simudzapeza chosintha m’machitidwe a Mulungu
63.Anthuamakufunsanizaola. Nenakuti,“Mulunguyekha ndiye amene amadziwa za ilo. Kodi chidzakudziwitsani ndi chiyani za olali? Mwinatu lili pafupi!”
66.Pa tsiku limene nkhope zawo zidzalangizidwe moto, iwo adzati, “Kukadakhala bwino kuti tikadamvera Mulungu ndi kumvera Mtumwi”
67.Ndipo iwo adzati, “Oh Ambuye wathu! Ndithudi ife tidamvera atsogoleri athu ndi akuluakulu athu kotero iwo adatisocheretsa.”
68.“oh Ambuye wathu! Apatseni iwo chilango chowirikiza ndipo atemberereni iwo ndi matemberero ochuluka.”
69.oh inu anthu okhulupirira! Musakhale ngati anthu amene adayankhula zinthu zoipa zokhudza Mose. Koma Mulungu adatsutsa zonse zimene anali kunena za Mose. Ndipo iye anali wolemekezeka kwa Mulungu
71.Iye adzasunga ntchito zanu pamalo abwino ndi kukukhululukirani machimo anu. Ndipo aliyense amene amamvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, iyeyo wapeza chinthu chopambana
72.Ndithudi Ife tidapereka udindo ndi chikhulupiriro kumwamba, pa dziko ndi pa mapiri koma zonse zidakana kulandira ndipo adauopa. Koma munthu adauvomera. Ndithudi iye ndi wosalungama ndiponso mbuli
73.Motero Mulungu adzalanga amuna ndi akazi a chinyengo. Ndiponso amuna ndi akazi opembedza mafano. Ndipo Mulungu adzakhululukira anthu onse okhululupirira, amuna ndi akazi. Mulungu ndi wokhululukira ndiponso mwini chisoni chosatha