الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Oh iwe Mtumwi! Opa Mulungu ndipo usamvere zonena za anthu osakhulupirira ndi a chinyengo. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha
37.Ndi pamene iwe udamuuza wina amene adalandira chisomo cha Mulungu ndi chifundo chake kuti, “Musunge mkazi wako ndipo uope Mulungu.” Ndipo iwe udabisa mu mtima mwako zimene Mulungu akadaulula ndipo iwe udaopaanthupamenekunalikoyenerakutiuziopaMulungu. Ndipo pamene Zaid adamusudzula iye, tidamukwatitsa iye kwa iwe ndi cholinga chakuti kutsogolo kusadzakhale vuto kwa anthu okhulupirira pa nkhani ya ukwati wokhudzana ndi ana owapeza pamene iwo asudzulana. Ulamuliro wa Mulungu uyenera kukwaniritsidwa
50.Oh iwe Mtumwi! Takulola kukhala ndi akazi onse amene iwe wapereka chiongo chawo ndi iwo amene ndi akapolo ako kuchokera kugulu limene lidagwidwa pankhondo ndipo Mulungu wakupatsa iwe; ana a akazi a atsibweni ndi azakhali ako, a kuchimuna kapena kuchikazi amene adachoka pamodzi ndi iwe. Ndiponso mkazi wina aliyense wokhulupirira amene adzipereka yekha kwa Mtumwi ngati Mtumwi afuna kumukwatira iye. Chilolezo ichi ndi cha iwe wekha osati cha anthu onse okhulupirira. Ife tikudziwa chimene tawasankhira iwo zokhudza akazi awo ndi akapolo amene iwo amasunga, ndi cholinga chakuti pasadzakhale vuto kwa iwe. Ndipo Mulungu amakhululukira nthawi zonse ndipo ndiye Mwini chisoni chosatha
53.Oh inu anthu okhulupirira! Musamalowe m’nyumba za Mtumwi pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kuti mukadye chakudya osati kukadikira chakudya mpaka pamene chiphikidwa. Koma pamene mwaitanidwa lowani ndipo pamene mumaliza kudya chokani. Musayembekeze kumvetsera nkhani. Ndithudi zimenezi zimamupatsa Mtumwi mavuto koma iye amachita nanu manyazi pamene Mulungu sachita manyazi kuulula choonadi. Ndipo ngati inu mufunsa katundu wina aliyense, funsani kuchokera ku malo osaonekera. Ichi ndi chabwino kwa inu ndiponso kwa iwo ndipo si koyenera kuti inu mumupatse mavuto Mtumwi wa Mulungu kapena kuti inu mukwatire akazi ake iye atawasiya. Ndithudi chimenechi ndi chinthu choipa pamaso pa Mulungu