لیل
الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja
1.
Paliusikupamenemdimaumayamba
2.
Ndimasanapamene kumayera
3.
Ndi pali Iye amene adalenga chachimuna ndi chachikazi
4.
Ndithudi zochita zanu zonse zili ndi mapeto osiyana
5.
Akakhala iye amene amapereka chaulere ndipo amamuopa Mulungu
6.
Ndipo amakhulupirira pochita zinthu zabwino
7.
Ife tidzamusalazira njira yake ya ku chipulumutso
8.
Koma iye amene sapereka chaulere ndipo amaganiza kuti ndi woima payekha
9.
Sakhulupirira ndipo sachita ntchito zabwino
10.
Tidzamusalazira njira yake ya ku chionongeko
11.
Kodi chuma chake chidzamuthandiza chiani pamene iye azidzazunzika
12.
Ndithudi ndi udindo wathu kupereka chilangizo
13.
Ndipo, ndithudi, zonse za m’moyo umene uli nkudza ndi za m’moyo uno ndi zathu
14.
Motero ndakuchenjezani za moto wa lawilawi
15.
Kulibe Al-Dhuha 655 munthu amene akapsye nawo kupatula munthu wochita zoipa
16.
Amene amakana choonadi ndipo safuna kumvera chenjezo
17.
Koma anthu onse olungama, adzatalikirana nawo
18.
Amene amapereka chaulere chake poonjezera kudziyeretsa
19.
Osati chifukwa chakuti afuna kupezako cholowa ayi
20.
Kupatula ndi cholinga chopeza chisomo cha Ambuye wake, wapamwamba mwamba
21.
Ndithudi iye adzasangalala
پچھلی سورہ
اگلی سورہ