الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Chidziwitso ichi chikhazikitsa malire oikidwa ndi Mulungu ndi Mtumwi wake, kwa anthu opembedza mafano amene mwapanga nawo lonjezo
74.Iwo amalumbira pali Mulungu kuti sanena china chilichonse. Koma iwo adalankhula mawu oonetsa kusakhulupirira ndipo iwo sanakhulupirire atalowa Chisilamu. Ndipo iwo anatsimikiza kuchita zimene sadathe kuzichita. Ndipo iwo sanathe kupeza chifukwa choyenera kuti atero kupatula kuti Mulungu ndi Mtumwi wake adawalemeretsa ndi katundu wake. Ngati iwo alapa, zikhala zabwino kwa iwo, koma ngati atembenuka, ndithudi, Mulungu adzawalanga ndi chilango chowawa pa dziko lino ndi mdziko limene lili nkudza. Iwo alibe wina aliyense Wowateteza padziko lapansi