غاشیہ
الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja
1.
Kodi wamva za chinthu chachikulu chimene chili nkudza
2.
Nkhope zina, patsiku limeneli, zidzachititsidwa manyazi
3.
Pogwira ntchito zotopetsa
4.
Iwo adzalowa kumoto woyaka
5.
Iwo adzapatsidwa madzi oti amwe kuchokera kuchitsime cha moto
6.
Sadzakhala ndi chakudya china koma chiphe cha mtengo waminga
7.
Chimene sichidzawapatsa thanzi kapena kuthetsa njala
8.
Nkhope zina, pa tsikuli, zidzakhala zosangalala
9.
Adzakondwa chifukwa cha ntchito zawo
10.
Atakhala m’minda ya pamwamba
11.
Kumene iwo sadzamva zoononga kapena za bodza
12.
Mudzakhala kasupe wa madzi oyenda
13.
Ndi mipando yonyamuka ya wofowofo
14.
Ndi zikho zomwera zitaikidwa pambali pake
15.
Ndi makushoni yoikidwa m’mizere
16.
Ndi mikeka yoyalidwa bwino pansi pake
17.
Kodi iwo saona mmene ngamira zidalengedwera
18.
Ndi Kumwamba mmene kudakwezedwera
19.
Ndi mapiri mmene adalengedwera mokhazikika
20.
Ndi dziko mmene adalitambasulira
21.
Motero akumbutse, chifukwa udindo wako ndi wowakumbutsa
22.
Iwe sindiwe munthu wowakakamiza ayi
23.
Kupatula iye Al Fajr 651 amene abwerera m’mbuyo ndi kuyamba kusakhulupirira
24.
Motero Mulungu adzamulanga chilango chachikulu
25.
Ndithudi onse adzabwerera kwa Ife
26.
Ndipo, ndithudi, chiwerengero cha zochita zawo chidzakhala kwa Ife