طارق
الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja
1.
Pali kumwamba ndi pali Nyenyezi yowala
2.
Kodi chidzakudziwitsa kuti Nyenyezi yowala ndi chiani
3.
Ndi Nyenyezi yowala kothobwetsa maso
4.
Ndithudi moyo uliwonse uli ndi mtetezi wake
5.
Tamulekani munthu kuti aganize kuti adalengedwa kuchokera ku chiyani
6.
Iye adalengedwa kuchokera ku madzi otuluka
7.
Amene amatuluka kuchokera pakati pa pfupa la munsana ndi nthiti
8.
Ndithudi Iye ali ndi mphamvu zomudzutsa
9.
Pa tsiku limene zinthu zobisika zidzayesedwa
10.
Ndipo adzakhala wopanda mphamvu kapena womuthandiza
11.
Pali mtambo umene umapereka mvula kawiri kawiri
12.
Ndi pali dziko lapansi limene limang’ambika
13.
Ndithudi! Awa ndi mawu amene amasiyanitsa
14.
Si nthabwala ayi
15.
Ndithudi iwo Al-A’la 649 ali kukonza chiwembu
16.
Ndipo Inenso ndili kukonza chiwembu
17.
Motero apatse nthawi anthu osakhulupirira. Ndipo chita nawo mwamtendere pa kanthawi kochepa