37.Ambuye wa Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, Mwini chisoni chosatha ndipo iwo sadzatha kulankhula naye
38.Patsiku limene Mzimu ndi angelo adzaima pa mizere ndipo palibe amene adzalankhula kupatula yekhayo amene adzalandira chilolezo cha Mwini chifundo chosatha ndipo adzanena chinthu chimene chili choona
39.Ndithudi tsiku limeneli ndi loona, motero iye amene afuna, mulekeni atsatire njira yobwerera kwa Ambuye wake
40.Ndithudi takuchenjezani za chilango chowawa chimene chili nkudza posachedwa. Tsiku limene munthu adzayang’ana ntchito zimene manja ake adatsogoza, ndipo osakhulupirira adzati: “Kalanga ine, ndikanakhala dothi.”