مرسلات
الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja
1.
Pali mphepo imene imatsatana pafupipafupi
2.
Pali mphepo ya mkuntho
3.
Pali mphepo imene imamwaza mitambo ndi mvula
4.
Pali mavesi amene amasiyanitsa chabwino
5.
Pali angelo amene amabweretsa chivumbulutso kwa Atumwi
6.
Kuthetsa kukangana kapena kuwachenjeza
7.
Ndithudi zonse zimene mwalonjezedwa zidzachitika
8.
Pamene nyenyezi zidetsedwa
9.
Ndi pamene thambo la kumwamba ling’ambika pakati
10.
Ndi pamene mapiri aphwanyika kukhala fumbi
11.
Ndi pamene Atumwi onse asonkhanitsidwa kukhala pamalo amodzi
12.
Kodi ndi tsiku liti limene izi zidzachitike
13.
Lidzakhala tsiku la chiweruzo
14.
Kodi ndi chiyani chidzakudziwitse zatsiku la chiweruzo
15.
Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
16.
Kodi Ife sitinaononge anthu a makedzana
17.
Kotero tidzaipanga mibadwo yotsatira kuti ione zomwezo
18.
Mmenemu ndi mmene timakhaulitsira anthu ochita zoipa
19.
Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
20.
Kodi sitidakulengeni inu kuchokera ku madzi onyozeka
21.
Amene tidasunga pamalo okhazikika
22.
Mpaka nthawi yake itakwana
23.
Motero Ife tinayesa ndipo Ife wodziwa kuyesa
24.
Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
25.
Kodi Ife sitinapange nthaka ngati malo okumaniranamo
26.
Amoyo ndi akufa
27.
Ndipo tidalenga Al Mursalat 635 mapiri atali pa dziko ndi kukupatsani madzi okoma kuti muzimwa
28.
Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
29.
(Zidzanenedwa kuti): “Pitani ku chilango chimene munkati sichidzabwera!”
30.
Pitani inu mu chithunzi, mu magulu atatu
31.
Opanda mthunzi kapena pokhala pokutetezani ku malawi a moto
32.
Ndithudi! Umatulutsa malawi ake akulu akulu ngati nyumba zachifumu
33.
Ndipo ooneka ngati ngamira ya chikasu
34.
Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
35.
Patsiku limeneli iwo sadzatha kulankhula
36.
Ndipo sadzaloledwa kuti apereke chidandaulo
37.
Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
38.
Limeneli ndilo tsiku la chiweruzo. Ife takusonkhanitsani nonse pamodzi ndi anthu a makedzana
39.
Tsopano ngati inu muli ndi chiwembu, chitani chiwembu chanu kwa Ine
40.
Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
41.
Ndithudi anthu angwiro adzakhala mu mthunzi wozizira ndi pa akasupe
42.
Ndi zipatso zimene afuna kukhosi kwawo
43.
Idyani ndipo imwani mosangalala chifukwa cha zimene mudachita
44.
Ndithudi, mmenemo ndi mmene timalipirira anthu angwiro
45.
Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
46.
Idyani ndipo musangalale kwa kanthawi kochepa. Ndithudi inu ndinu oipa kwambiri
47.
Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
48.
Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Weramani.” Iwo amakana kutero
49.
Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
50.
Kodi ndi Uthenga uti woposa uwu umene adzaukhulupirire