2.Ndithudi Ife tidamulenga munthu kuchokera ku madontho a umuna umene unasakanizidwa ndi ukazi ndi cholinga chomuyesa motero Ife tidamupanga iye kukhala wakumva ndi woona
5.Ndithudi anthu onse angwiro adzamwa chakumwa chosakanizidwa ndi madzi ochokera pa kasupe wa ku Paradiso chotchedwa Kafur
7.Iwo amene amakwaniritsa malonjezo awo ndipo amakhala ndi mantha ndi tsiku limene zoipa zidzasefukira ponseponse
8.Ndipo amapereka chakudya chifukwa cha chikondi cha Mulungu, kwa anthu aumphawi, amasiye ndi kwa akaidi
9.Ife tili kukudyetsani chifukwa cha Mulungu basi. Ife sitifuna malipiro kapena mayamiko kuchokera kwa inu
10.Ndithudi ife tiopa tsiku loopsa ndi laululu limene lidzasanduliza nkhope kuoneka monyasa, limene lili nkudza kuchokera kwa Ambuye wathu
11.Motero Mulungu awapulumutsa iwo ku zoipa za tsiku limeneli ndi kuwapatsa nyali yokongola kuti akhale mosavutika ndi mwachisangalalo
13.Ali kukhala m’Paradiso, pamipando yawofowofo, iwo sadzamva kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira kwambiri
14.Ndipo mithunzi idzakhala pafupi ndi iwo ndipo zipatso zidzalendewera mu matsanzi kuti asamavutike pothyola
16.Matambula oonetsa zinthu zomwe zili m’kati mwake, opangidwa kuchokera ku siliva. Iwo adzathiramo chakumwa molingana ndi chilakolako chawo
19.Ndipo adzazunguliridwa ndi ana owatumikira a misinkhu yofanana. Ndipo ngati iwe utawaona ukhoza kuganiza kuti ndi ndolo zomwazikamwazika
21.Iwo adzavala nsalu zokongola za silika zooneka ngati msipu zopetedwa ndi golide. Iwo adzavala zibangiri za siliva ndipo Ambuye wawo adzawapatsa chakumwa chabwino
24.Motero pirira ndipo tsatira malamulo a Ambuye wako ndipo usamvere zonena za munthu wochimwa kapena wosakhulupirira amene ali pakati pawo
27.Ndithudi! Awa amakonda kwambiri moyo wa msanga msanga wa masiku ano, ndipo amaiwala tsiku limenelidzakhalalovuta
28.Ndifeamenetidawalengandipo tinaika mphamvu m’ziwalo zawo. Koma ngati Ife titafuna, tikhoza kulenga anthu ena kuti alowe m’malo mwawo
29.Ndithudi! Ili ndi chenjezo motero aliyense amene afuna, mulekeni kuti atsatire njira yoyenera yopita kwa Ambuye wake
30.Koma inu simudzatha kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu. Ndithudi Mulungu ndiye Mwini kudziwa ndi Mwini nzeru
31.Iye adzaonetsa chisomo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma anthu ochimwa, Iye wawakonzera iwo chilango chowawa