الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.ohiweamenewakutidwa
31.Ife sitidasankhe wina aliyense koma angelo kuti aziyang’anira moto ndipo tinakhazikitsa chiwerengero chawo ngati mayesero kwa anthu osakhulupirira, kuti iwo onse amene alandira mawu a Mulungu akhulupirire ndi kuti anthu okhulupirira m’choonadi apitirize chikhulupiriro chawo; kuti iwo amene adalandira kale mawu a Mulungu ndiponso anthu onse okhulupirira moona asakhale ndi chikaiko china chilichonse; ndipo kuti onse amene m’mitima mwawo muli matenda pamodzi ndi anthu osakhulupirira anganene kuti: “Kodi Mulungu afuna kutanthauza chiyani pa chitsanzo chotere?” Mmenemo ndi mmene Mulungu amasokeretsera munthu aliyense amene Iye wamufuna ndi kutsogolera aliyense amene Iye wamufuna. Palibe munthu amene amadziwa asirikali a Ambuye wako kupatula Iye mwini. Ichi si china chilichonse koma chikumbutso kwa anthu onse