الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Oh iwe amene wadzikulunga m’chovala
20.NdithudiAmbuye wako amadziwa kuti nthawi zina iwe umakhala tcheru mphindi ziwiri pakati pa mphindi zitatu za usiku, mwina theka la usiku ndipo nthawi zina mphindi imodzi pakati pa mphindi zitatu za usiku, monga momwe gulu lina la anthu amene ali nawe. Ndipo Mulungu ndiye amene amasiyanitsa usiku ndi usana. Iye amadziwa kuti siungathe kupemphera mphindi zonse ndipo wakuyang’ana mwachisoni. Kotero lakatula magawo ena a Korani amene angakhale apafupi kwa iwe. Iye amadziwa kuti pakati panu pali anthu odwala ndi ena amene ali kupita uku ndi uku padziko kufunafuna zokoma za Mulungu ndi ena amene ali kumenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Motero lakatula, mawu a m’Korani, amene ungathe kulakatula, ndipo pitiriza kupemphera ndipo pereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo kongoza ngongole yabwino kwa Mulungu ndipo chabwino chilichonse chimene muli kutsogoza, mudzachipeza kwa Mulungu, chitasungidwa bwino ndipo mudzalandira mphotho ya mtengo wapatali kuchokera kwa Iye. Ndipo pempha chikhululukiro kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha