4.“Iye adzakukhululukirani machimo anu ndi kukusungani bwino mpaka nthawi ya imfa yanu. Ndithudi nthawi ya Mulungu ikakwana, palibe wina aliyense amene angaibwezere m’mbuyo inu mukadadziwa.”
7.“Ndipo, ndithudi, nthawi yonse imene ndiitana kuti Inu muwakhululukire, iwo amatenga zala zawo ndi kutseka m’makutu mwawo ndipo amatenga mikhanjo yawo ndi kufunditsa kumutu kwawo ndipo amapitirirabe kuchita zoipa monyada.”
21.Nowa adati: “oh Ambuye! Anthu anga sali kundimvera ine koma mmalo mwake ali kutsatira amene sangawaonjezere chuma ndi ana koma mavuto.”
23.Ndipo ati: “Mwanjira ina iliyonse inu musaleke kupembedza milungu yanu. Musaleke kupembedza Wadd, Suwa, Yaghuth, Yauq kapena Nasr.”
24.“Ndipo, ndithudi, iwo asocheza anthu ambiri. Ndipo Inu musaonjeze china chili chonse kwa anthu ochita zoipa chifukwa apitirizabe kuchita zoipa.”
25.Chifukwa cha machimo awo iwo anamizidwa ndipo adaponyedwa ku moto ndipo iwo sanapeze wina aliyense kuti awathandize, m’malo mwa Mulungu
27.“Ngati Inu muwasiya iwo adzasocheretsa akapolo anu okhulupirira ndipo iwo adzabereka anthu ochita zoipa ndi osakhulupirira.”
28.“Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi iye amene alowa mnyumba yanga ngati wokhulupirira ndiponso okhulupirira onse amuna ndi akazi. Ndipo kwa anthu osakhulupilira, Inu musawaonjezere china koma chionongeko