الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Alif Lam Mim Sad
143.Ndipo pamene Mose adabwera panthawi ndi malo osankhidwa ndi Ife, Ambuye wake adalankhula naye ndipo iye adati: “Oh Ambuye wanga! Dzionetseni inu kwa ine kuti ndikuoneni.” Mulungu adati: “Iwe siudzandiona Ine ayi. Koma uone kuphiri ndipo ngati ilo lingakhalebe chikhalire ndiye kuti ukhoza kundiona Ine.” Ndipo pamene Ambuye wake anadzionetsera pa phiri, phiri lidaphwanyika ndi kusanduka fumbi lokhalokha ndipo Mose adagwa pansi ndipo adakomoka koma pamene anatsitsimuka iye adati: “Ulemerero ukhale kwa Inu. Ine ndalapa kwa Inu ndipo ine ndine woyamba wa anthu okhulupirira.”
150.Ndipo pamene Mose adabwerera kwa anthu ake, wokwiya ndi wachisoni, iye adati: “Kodi ndi chinthu choipa bwanji chimene mwachita pamene ine kudalibe! Kodi inu munafulumira ndi kusiya kupembedza Ambuye wanu?” Ndipo iye adaponya pansi matabwa a malamulo, nagwira mutu wa m’bale wake ndi kumukokera kwa iye. Aroni adati: “Iwe mwana wa Amayi anga! Ndithu anthu awa adandiposa mphamvu ndipo adakhala pang’ono kundipha ndipo usalole kuti adani anga asangalale pa ine ndipo usandiike pa gulu la anthu ochita zoipa.”
155.Ndipo Mose adasankha, pakati pa anthu ake, amuna makumi asanu ndi awiri kuti adzakumane nafe ndipo pamene nthaka idagwedezeka pamapazi pawo, Mose adati: “Chikadakhala chifuniro chanu, Ambuye, mukadawaononga iwo ndi ine kale. Kodi inu mungationonge chifukwa cha ntchito za anthu amene ali pakati pathu? Awa ndi mayesero anu, amene Inu mumasocheretsa aliyense amene mwamufuna ndi kutsogolera yemwe mwamufuna. Inu nokha ndinu Mtetezi wathu ndipo tichitireni chisoni chifukwa Inu ndinu wopambana onse amene amakhululukira.”
157.Iwoameneamatsatira Mtumwi kapena Mneneri amene sadziwa kulemba ndi kuwerenga, amene mbiri yake inalembedwa m’Buku la chipangano chakale ndi mu chipangano chatsopano. Iye amawalamulira kuchita zabwino ndipo amawaletsa kuchita zoipa. Ndipo amawaloleza zabwino ndi kuwaletsa zonyansa. Iye amawapeputsira katundu wolemera amene adali pa iwo. Motero iwo amene akhulupirira mwa iye ndi kumulemekeza, ndi kumuthandiza iye ndi kutsata kuunika kumene kwatumizidwa ndi iye, ndi okhawo amene adzakhala opambana
169.Ndipo lidalowa m’malo gulu lina loipa limene linatenga Buku, koma iwo adasankha zinthu zopanda pake za pa dziko lapansi. Ndipo iwo adati “Tidzakhululukidwa.” Koma zitawapezanso zinthu zopanda pake za mtundu womwewo iwo akadazilandira. Kodi lonjezo la m’Buku silinalandiridwe kuchokera kwa iwo kuti sadzanena chili chonse chokhudza Mulungu kupatula choonadi? Ndipo iwo aphunzira zomwe zili m’menemo. Ndipo dziko limene lili nkudza ndi labwino kwa anthu oopa Mulungu. Kodi inu mulibe nzeru