7.Ndithudi Ambuye wako amadziwa bwino amene wasochera ku njira yake ndipo amadziwa bwino amene amayenda m’njira yoyenera
17.Ndithudi Ife tidawayesa iwo monga momwe tidawayesera eni ake a munda, amene adalumbira kuti adzakolola mbewu zawo m’mawa mwake
19.Kotero kudadutsa china chake chochokera kwa Ambuye wako nthawi ya usiku ndi kuwotcha pamene iwo anali kugona
28.wangwiro amene anali pakati pawo adati: “Kodi ine sindidakuuzeni kuti bwanji inu simunena kuti: Ngati Mulungu alola?”
32.“Mwina kuti Ambuye wathu adzatipatsa munda wina wabwino m’malo mwa uwu. Ndithudi ndi kwa Iye kumene timapempha modzichepetsa.”
33.Chimenechi ndicho chilango koma ndithudi chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chowawa kwambiri, iwo akadadziwa
39.Kapena inu mwalandira kuchokera kwa Ife, lonjezo lotsimikizika mpaka pa tsiku louka kwa akufa kuti, ndithudi, inu mudzapeza zimene mukufuna
42.Ndipatsikulimenechinthuchoopsachidzachitika, iwo adzaitanidwa kuti apembedze, koma adzalephera kutero
43.Maso awo adzayang’ana pansi ndipo adzanyozedwa kwambiri chifukwa iwo adauzidwa kupembedza pamene adali pa mtendere
44.Kotero ndisiyire aliyense amene akutsutsana ndi chenjezo ili. Ife tidzawalanga pang’onopang’ono m’njira imene iwo saizindikira
48.Motero pirira podikilira chiweruzo cha Ambuye wako ndipo usakhale ngati amene adamezedwa ndi nsomba pamene adalira kupempha chithandizo iye ali m’mavuto
49.Ngati Ambuye wake akadapanda kumuonetsa chisomo chake, ndithudi iye akadakhalabe koma iye adaponyedwa pa mtunda pamene anali wolakwa
51.Ndipo, ndithudi, iwo onse osakhulupirira akadakusokeretsa ndi maso awo pamene amakumbutsidwa ndipo amati: “Ndithudi uyu ndi Wamisala.”