2.Iye amene adalenga imfa ndi moyo kuti akhoza kukuyesani inu kuti ndani wa inu amene wasunga malamulo onse mwaubwino. Ndipo Iye ndi Wamphamvu ndi Wokhululukira
3.Iye ndi amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake. Inu simungaone cholakwa china chilichonse mu chilengedwe cha Mwini chisoni chosatha. Tapenyetsetsani! Kodi inu mungaone cholakwika china chilichonse
5.Ndithudi Ife takongoletsa thambo loyamba ndi nyali ndipo tazipanga nyalizo ngati mipaliro yothamangitsira Satana ndipo tawakonzera iwo chilango chamoto woyaka
6.Ndipo iwo amene sakhulupirira mwa Ambuye wawo, kuli chilango cha kumoto ndipo chimaliziro chawo chidzakhala choipa
8.Pafupifupi kuphulika chifukwa cha kukwiya. Ndipo nthawi zonse pamene gulu liponyedwamo, amene amayang’anira moto adzafunsa kuti: “Kodi panalibe wina aliyense amene adadza kwa inu kudzakuchenjezani?”
9.Ndipo iwo adzati: “Inde. Ndithudi Mchenjezi adadza kwa ife koma tidamukana ndipo tinkati: Mulungu sadavumbulutse china chilichonse ndipo iwe ndiwe wosokoneza kwambiri.”
10.Ndipo iwo adzati: “Tikadakhala kuti tidamvera kapena kuganiza bwino, ife sitikadakhala m’gulu la anthu opita ku moto.”
12.Ndithudi! Iwo amene amaopa Ambuye wawo ngakhale samuona, ndithudi, iwo adzawakhululukira machimo awo ndipo adzalandira mphotho ya mtengo wapatali
14.Kodi Iye amene adalenga zinthu zonse asadziwe? Ndithudi Iye ndi wa Chisoni chosatha ndi Mwini kudziwa chili chonse
15.Iye ndiye amene anakukonzerani dziko, motero pitani paliponse mu ilo, ndipo idyani zokoma zake zimene wakupatsanindipondikwaIyekumenezonsezidzabwerera
16.Kodi inu mumaganiza kuti ndinu wokhazikika moti Iye amene ali pamwamba pa kumwamba sangathe kung’amba nthaka imene ili pansi panu kuti ikumezeni? Taonani! Ili kugwedezeka
17.Kapena mumaganiza kuti inu ndinu okhazikika kuposa zimene zili kumwamba kuti Iye sangathe kukutumizirani mphepo ya mkuntho? Kotero inu mudzadziwa kuopsa kwa chenjezo langa
19.Kodiiwosaonambalamezimenezimaulukapamwamba pawo, zikutambasula ndi kutseka mapiko awo? Palibe chimene chimazigwira kupatula Mwini chisoni chosatha. Ndithudi Iye amaona chilichonse
20.Kodi ndani amene angakuthandizeni inu kupatula Mwini chisoni chosatha? Anthu onse osakhulupirira ndi olakwa
21.Kodi ndani amene angakupatseni chisamaliro ngati Iye atakaniza chisamaliro chake? Koma iwo amapitiriza kuchita mtudzu ndi kugalukira
22.Kodi iye amene amayenda osaona ndi ofanana ndi amene walangizidwa kapena amene amayenda mu njira yoyenera
23.Nena: “Ndiye amene adakulengani inu ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Inu simuthokoza kawirikawiri.”
27.Koma pamene iwo adzachiona chili nkudza pafupi, nkhope za anthu osakhulupirira zidzakhala za chisoni ndipo kudzanenedwa kuti: “Ichi ndi chimaliziro chimene munkafunsa kuti chidzafika liti?”
28.Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati Mulungu atandiononga ine pamodzi ndi iwo amene ali nane, ngakhale kuti Iye adzaonetsa chifundo pa ife, ndani amene angateteze anthu osakhulupirira ku chilango chowawa?”
29.Nena: “Iye ndi Mwini chifundo chosatha, mwa Iye ife timakhulupirira ndipo mwa Iye ife timaika chikhulupiriro chathu. Kotero inu mudzadziwa posachedwapa kuti ndani amene ali wochimwa.”