الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Oh iwe Mtumwi! Ngati usudzula akazi ako, asudzule potsatira nthawi zawo. Ndipo werenga bwino bwino masiku awo. Ndipo opani Mulungu Ambuye wanu ndipo musawapirikitse m’nyumba zawo ndipo iwo asachoke pokhapokha ngati iwo apalamula mlandu wachigololo. Amenewa ndiwo malamulo amene akhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene aphwanya malamulo a Mulungu, ndithudi, amapondereza mzimu wake. Inu Al Talaq 605 simudziwa kuti, mwina, Mulungu adzakukumanizaninso