الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukhazikitsa mdima ndi kuwala, komabe anthu osakhulupirira amakhazikitsa milungu ina kuti ndi yolingana ndi Ambuye wawo
70.Apewe iwo amene amasandutsa chipembedzo chawo kukhala masewera kapena nthabwala ndipo asokonezeka ndi zokoma za moyo wa dziko lapansi. Koma achenjeze ndi ilo kuti ungadzaonongeke mzimu wawo chifukwa cha zimene udachita pamene siudzakhala ndi wousamalira kapena kuwuteteza kupatula Mulungu, ndipo ngakhale iwo apereka chuma chopepesera, sichidzalandiridwa konse. Otere ndiwo amene aonongedwa chifukwa cha zimene anachita. Iwo adzalandira zakumwa zowira ndi chilango chowawa chifukwa cha zinthu zimene sadakhulupirire
93.Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lonamizira Mulungu kapena amati: “Ine ndalandira chibvumbulutso pamene sichidavumbulutsidwe kwa iye chilichonse?” Kapena munthu amene amati: “Ine ndikhoza kuvumbulutsa zinthu zofanana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa?” Ndipo iwe ukadangoona anthu ochimwa pamene ali kufa ndi pamene angelo ali kutambasula manja awo akuti: “Perekani mizimu yanu. Inu mudzalipidwa mphotho yochititsa manyazi lero chifukwa cha zimene munali kunena zabodza zokhudza Mulungu. Ndiponso inu munali kukana chivumbulutso chake mwa mwano.”
99.Iye ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumwamba ndipo ndi iyo, Ife timameretsa mbewu zosiyana siyana ndipo kuchokera ku izo timatulutsa mphesi za ziwisi zimene zimabereka mbeu mothinana. Ndipo kuchokera ku mitengo ya tende kumadza zipatso za tende zotsika pansi, minda ya mphesa ndi mitengo ya mafuta ya azitona, chimanga cha chizungu, zipatso zofanana koma zosiyanasiyana. Taonani zipatso zake pamene zili kubereka, kukhwima ndi kumapsya. Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira