الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi wanzeru
2.Ndiye amene adachotsa anthu osakhulupirira amene adali pakati pa anthu a m’Buku kuchokera ku nyumba zawo pamene adakumana poyamba. Iwe sumaganiza ndi pang’ono pomwe kuti angachoke. Ndipo iwo anali kuganiza kuti Malinga awo adzawateteza kwa Mulungu! Koma chilango cha Mulungu chidadza pa iwo kuchokera kumbali imene iwo sanali kuyembekezera. Ndipo Iye adaika mantha m’mitima mwawo kotero iwo adagwetsa nyumba ndi manja awo ndiponso manja a anthu okhulupirira. Motero chenjerani tsopano inu amene muli ndi maso