الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Ndithudi Mulungu wamva mau a mkazi amene ali kutsutsana ndi iwe pa nkhani ya mwamuna wake ndipo iye wapereka madandaulo ake kwa Mulungu. Ndipo Mulungu wamva kukangana kwanu chifukwa Iye amamva ndiponso amaona chili chonse
8.Kodi iwe siudawaone amene adaletsedwa kuchita misonkhano ya mseri komabe amayambanso kuchita misonkhano ya chinsinsi imene adaletsedwa kuti asamachite? Iwo amachita misonkhano pakati pawo ndi cholinga choukira ndi kusamvera Mtumwi wa Mulungu. Koma iwo akamadza kwa iwe, iwo amakulonjera iwe osati monga mmene Mulungu amakulonjerera ayi koma mwachinyengo. Ndipo iwo amati kwa wina ndi mnzake: “Kodi bwanji Mulungu satilanga pa zimene timanena?” Gahena ndi yokwana kwa iwo, ndipo adzapsa m’malawi ake. Ndipo kumeneko ndi konyansa kwambiri
22.Iwe sudzapeza anthu amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ali kuchita chibwenzi ndi iwo amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake ngakhale kuti atakhala abambo wawo, kapena ana awo kapena abale awo kapena anansi awo. Kwa awa, Iye wakhazikitsa chikhulupiriro m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi ulangizi, wochokera kwa Iye. Ndipo Iye adzawalandira m’minda ya Paradiso, imene pansi pake pamayenda mitsinje kuti akhale komweko mpaka kalekale. Mulungu wasangalala nawo ndipo nawonso asangalala ndi Iye. Iwo ndi anthu a gulu la Mulungu. Ndithudi ndi anthu a Mulungu amene adzapambana