الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Chilichonse chimwe chili kumwamba ndi padziko lapansi chimalemekeza Mulungu. Iye ndiye Mwini mphamvu, Mwini nzeru
20.Dziwani kuti moyo wa padziko lino lapansi ndi masewera ndi wotailako nthawi, chionetsero ndi kunyada ndi mpikisano pakati pa wina ndi mnzake wofuna chuma ndi ana. Fanizo lake lili ngati mvula ndi zomera zimene zimadza chifukwa cha zimene zimabweretsa chisangalalo kwa ozilima. Pasanapite nthawi izo zimafota ndi kuoneka za chikasu. Ndipo zimauma ndi kugwa pansi. Koma m’moyo umene uli kudza, kuli chilango chowawa kwa anthu ogona m’machimo ndi chikhululukiro chochokera kwa Mulungu ndiponso chisangalalo chake kwa iwo amene amadzipereka kwa Mulungu. Kodi moyo wa padziko lino lapansi ndi chiyani kupatula chinyengo chabe