3.Iwo amakana choonadi koma amatsatira zilakolako zawo. Koma chinthu chilichonse chili ndi kumaliza kwake
9.Asanadze iwo, anthu a Nowa adakana kapolo wathu ndipo adati, “Uyu ndi munthu wamisala.” Ndipo iwo adamuthamangitsa iye ndi kumunyoza kwambiri
17.Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulidziwa ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
22.Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
24.Iwo adati, “Munthu! Mmodzi yekha wochokera ku mtundu wathu kuti timutsatire? Ndithudi ife tikhala olakwa kwambiri ndiponso a misala.”
25.“Kodi ndiye kuti uthenga waperekedwa kwa iye yekha pakati pa ife tonse? Iyayi! Iye ndi wabodza ndi wodzikweza.”
27.Ndithudi Ife titumiza ngamira yaikazi ngati mayesero kwa iwo. Motero iwe uwapenyetsetse ndipo ukhale wopirira
31.Ndithudi tidawatumizira mfuwu umodzi ndipo onse adali ngati nkhuni zodula zimene munthu womanga mpanda amatola
32.Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
34.Ndithudi Ife tidawatumizira mphepo yonyamula miyala kupatula a pa banja la Loti amene tidawapulumutsa mu ola lomaliza la usiku
37.Ndipo, ndithudi, iwo adafuna kuchititsa manyazi alendo ake. Motero Ife tidawachititsa khungu. Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga
40.Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
43.Kodi anthu anu osakhulupirira ndi abwino kuposa awa? Kapena inu muli ndi chitetezo mu m’mawu a Mulungu
46.Iyayi, koma ola lachiweruzo ndi nthawi imene iwo adalonjezedwa ndipo ola limeneli lidzakhala loopsa kwambiri
48.Tsiku limene iwo adzaduduluzidwa pa nkhope zawo kunka ku moto, (zidzanenedwa) “Lawani ululu wa ku Moto.”