2.Koma iwo alikudabwa kuti kwa iwo kwadza mchenjezi wochokera pakati pawo. Motero anthu osakhulupirira amati, “chimenechi ndi chinthu chachilendo!”
6.Kodi iwo sayang’ana kumwamba ndi kuona mmene tidakukonzera ndi kukukongoletsera ndi kuona kuti kulibe mipata
7.Ndipo dziko lapansi Ife talipanga kukhala losalala ndi kuikamo mapiri ndipo tidameretsa mu dzikolo mbewu zokongola zosiyanasiyana
9.Ndipo timatumiza kuchokera ku mitambo mvula yodalitsika ndipo timameretsa m’minda mbewu zimene zimakololedwa
11.Chakudya cha akapolo. Ndipo Ife timapereka moyo kunthaka imene idali yakufa. Kumeneko ndiko kuuka kwa akufa
14.Ndi iwo amene anali kukhala m’nkhalango ndi anthu a ku Tuba, aliyense wa iwo adakana Atumwi ndipo chenjezo langa lidakwaniritsidwa
15.Kodi Ife tidatopa ndi chilengedwe choyamba? Iyayi. Iwo asokonezeka ndi nkhani zokhudza chilengedwe chatsopano
16.Ndithudi Ife tidamulenga munthu ndipo timadziwa zimene mtima wake umamuuza. Ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wa moyo wake
19.Ndipo ululu wa imfa udzadza pa iye mwachoonadi. Ichi ndicho chimene iwe unali kuyesetsa kuchithawa
22.(Ndipo kudzanenedwa kwa anthu ochimwa) kuti, “Ndithudi inu simudafune kuchenjezedwa za chimenechi ndipotsopano Ifetavundukulachimenechimakuphimbani. Ndipo lero maso anu ali kuona zenizeni.”
26.“Iye amene anali kukhazikitsa milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, motero mponyeni ku chilango chowawa.”
27.Mnzake adzanena kuti, “Ambuye wathu! Ine sindidamuuze kuti aziswa malamulo ayi koma iye adadzisocheretsa yekha.”
30.Patsiku limene Ife tidzaifunsa Gahena kuti, “Kodi mwadzadza?” Ndipo iyo idzati, “Kodi akanalipobe ena?”
32.Ichi ndicho chimene mudalonjezedwa ndipo ndi mphotho kwa iye amene amadzipereka kwa Mulungu nthawi zonse nasunga malamulo ake
33.Ndiponso kwa iye amene amaopa Mwini chisoni chosatha wosaoneka ndipo amadza kwa Iye ndi mtima wodzichepetsa
36.Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaiononga iwo asanabadwe amene adali ndi mphamvu zoposa iwo ndipo iwo adafuna chitetezo padziko? Kodi iwo anali ndi kwina kothawira
37.Ndithudi muli chikumbutso mu zimenezi kwa iye amene ali ndi mtima kapena amatchera khutu pamene achenjezedwa
38.Ndithudi Ife tidalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi ndipo sitidatope ayi
39.Kotero pirira pa zonse zimene amanena ndipo lemekeza Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe
44.Tsiku limene dziko lidzang’ambika ndipo iwo adzatuluka mofulumira. Kumeneko ndiko kudzakhala kusonkhanitsidwa pamodzi
45.Ife timadziwa zonse zimene amanena ndipo iwe si ndiwe wankhanza ayi. Koma muchenjeze ndi Korani kwa aliyense amene aopa chilango changa