الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Ha Mim
15.Ndipo Ife tidalamula munthu kuti azichita zabwino kwa makolo ake. Amayi ake amavutika pomubereka ndi pomulera iye. Ndipo kuyambira pamene waberekedwa ndi pamene asiya kuyamwa ndi miyezi makumi atatu. Patapita nthawi iye amakula ndipo akakwanitsa zaka makumi anayi amati, “Ambuye wanga! Ndipatseni mphamvu ndi nzeru kuti ndikhale woyamika chifukwa cha chisoni chimene mwandionetsera ndi chimene mwaonetsera kwa makolo angakutindizichitazabwinozimenezidzakukondweretsani Inu. Ndipo chitireni zabwino zokhudza ana anga. Ndithudi ine ndiyang’ana kwa Inu polapa ndipo, ndithudi, ine ndine mmodzi wa anthu ogonjera.”