3.Ndi Buku limene mawu ake ndi ofotokozedwa mwatsatanetsatane. Ndi Korani ya m’chiyankhulo cha Chiarabu, kwa anthu ozindikira
4.Lopereka nkhani yabwino ndi chenjezo koma ambiri a iwo amabwerera m’mbuyo kotero sakumva chilichonse
5.Ndipo iwo amati, “Mitima yathu ndi yokutidwa ku zimene iwe uli kutiitanira ndipo makutu athu ndi ogontha ndipo chotchinga chili pakati pathu ndi iwe kotero iwe gwira ntchito yako ndipo nafenso tili kugwira yathu.”
6.Nena, “Ine ndine munthu monga inu nomwe. Koma zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi yekha kotero tsatirani njira yoyenera yopita kwa Iye ndipo pemphani chikhululukiro chake. Tsoka kwa iwo amene amafanizira milungu ina ndi Mulungu weniweni.”
9.Nena, “Kodi, ndithudi, inu muli kumukana Iye amene adalenga dziko lapansi m’masiku awiri ndipo muli kumufanizirandienakukhalaofanananaye? IyendiAmbuye wa zolengedwa zonse.”
10.Iye adaika mu dziko lapansi mapiri okhazikika pamwamba pake ndipo adalidalitsa ilo ndi kulipatsa chakudya, chokwanira chilichonse m’masiku anayi ofanana
11.Ndipo atatero Iye adabuka kumwamba pamene kudali nkhungu ndipo Iye adati adayankhula mawu okhudza kumwamba ndi ku dziko lapansi kuti, “Idzani nonse mwanokha kapena mokakamizidwa.” Onse adati, “Tibwera mosakakamizidwa.”
12.Ndipo Iye adakonza ndi kulenga maiko asanu ndi awiri m’masiku awiri ndipo adapereka ku dziko lililonse ulamuliro. Ndipo Ife tidaika ku muyamba wapansi nyenyezi zokongola kuti zizilonda. Umenewo ndi ulamuliro wa Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru
13.Koma ngati iwo abwerera m’mbuyo, nena, “Ine ndakuchenjezani inu za chilango chonga ngati chimene chidadza pa anthu a Aad ndi Thamoud.”
14.Ndipo pamene Atumwi awo adadza kwa iwo kuchokera ku mbali zonse, nati, “Musapembedze wina aliyense koma Mulungu.” Iwo adati, “Ngati Ambuye wathu akadafuna, Iye ndithudi, akadatumiza Angelo. Kotero ife, ndithudi, sitikhulupirira zimene inu mwatumidwa.”
15.Akakhala anthu a Aad, iwo adanyada kopambana padziko ndipo adati, “Kodi ali ndi mphamvu zopambana zathu ndani?” Kodi iwo saona kuti Mulungu amene adawalenga, ali ndi mphamvu zambiri zoposa zawo? Ndipo iwo anali kukana chivumbulutso chathu
16.Kotero Ife tidawatumizira mphepo yamkuntho m’masiku a tsoka, ndi cholinga choti alawe chilango chochititsa manyazi m’dziko lino koma, ndithudi, chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chochititsa manyazi zedi ndipo iwo sadzathandizidwa ayi
17.Akakhala anthu a Thamoud Ife tidawalangiza njira yoyenera koma iwo adasankha kuchita zoipa m’malo mochita zabwino kotero kwa iwo kudadza chilango chochititsa manyazi chifukwa cha ntchito zawo
19.Ndipo pa tsiku limene adani ake a Mulungu adzasonkhanitsidwa kupita kumoto, iwo adzaikidwa m’magulumagulu
20.Mpaka pamene wo atafika ku malo a moto makutu awo, maso awo ndi makungu awo adzapereka umboni wowaneneza pa zimene anali kuchita
21.Ndipo iwo adzati kwa makungu awo, “Bwanji inu muli kupereka umboni wotineneza?” Iwo adzati, “Mulungu, amene amayankhulitsa chilichonse, watiyankhulitsa ife ndipo Iye ndiye amene adakulengani inu poyamba ndipo nonse mudzabwerera kwa Iye.”
22.Ndipo inu simunadzibise ku makutu anu, maso anu ndi makungu anu kuti zisadzapereke umboni wokunenezani koma inu mumaganiza kuti Mulungu sadziwa zonse zimene munali kuchita
23.Ndipo ndi maganizo anu amene inu munali kuganiza okhudza Ambuye wanu amene wakubweretsani ku chionongeko tsopano muli m’gulu la anthu otayika
24.Ndipo ngati iwo apirira komabe ku moto ndiko kudzakhala kumalo kwawo. Ndipo ngati apempha chikhululukiro pempho lawo lidzakanidwa
25.Ndipo Ife tawasankhira anzawo amene adapanga kuti aziona zopusa zakale ndi zatsopano kukhala zinthu zokondweretsa kwa iwo. Ndipo chiweruzo chimene chidadza ku mtundu wa majini ndi kwa anthu amene adalipo kale chakwaniritsidwa kwa iwo. Ndithudi iwo ndi otayika kwambiri
26.Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Musamvetsere Koraniyi koma m’malo mwake muzipanga phokoso kuti mwina mukhoza kuigonjetsa.”
27.Koma, ndithudi, Ife tidzawalawitsa anthu osakhulupirira chilango chowawa, ndipo, ndithudi, Ife tidzawalipira chifukwa cha ntchito zawo zoipa zimene anali kuchita
28.Amenewo ndiwo malipiro a adani a Mulungu. Moto ndiwo malo awo a nthawi zonse. Malipiro okwanira malinga ndi ntchito zawo zoipa zimene anali kuchita pokana zizindikiro zathu
29.Ndipo iwo osakhulupirira adzati, “Ambuye wathu! Tilangizeni iwo amene ali pakati pa majini ndi anthu amene adatisocheretsa ife ndipo ife tidzawapondaponda ndi mapazi athu kuti iwo akhale a pansi kwambiri.”
30.Ndithudi iwo amene amati, “Ambuye wathu ndi Mulungu ndipo amapitiriza kutsatira njira yoyenera.” Kwa iwo angelo amadza nati, “Musaope ndipo musadandaule ayi. Koma landirani nkhani yabwino yokhudza Paradiso imene inu mudalonjezedwa!”
31.Ife tinali abwenzi anu m’moyo uno ndiponso ndi m’moyo umene uli nkudza. M’menemu inu mudzapeza chilichonse chimene mufuna ndipo m’menemo inu mudzalandira chilichonse chimene mupempha
32.Mphatso yamtengo wapatali yachokera kwa Iye amene amakhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha
33.Kodi amayankhula bwino ndani kuposa iye amene amati; ‘Ambuye wanga ndi Mulungu’ amaitanira anthu kunjira ya Mulungu amene amachita ntchito zabwino ndipo amati, “Ine ndine mmodzi wa Asilamu?”
34.Ntchito zabwino ndi ntchito zoipa sizifanana. Kotero gonjetsani choipa pochita chabwino ndipo, ndithudi, iye amene ali mdani wako adzakhala ngati bwenzi lako lapamtima
35.Koma palibe wina amene adzalandira zimenezi kupatula yekhayo amene amapirira kwambiri ndipo amadziletsa. Ndipo palibe wina amene angalandire kuposa iwo amene ali ndi mwayi wochuluka
36.Ndipo ngati iwe uyesedwa ndi Satana, funafuna chitetezo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye amene amamva ndipo amadziwa chinthu china chilichonse
37.Ndipo pakati pa zizindikiro zake pali usiku ndi usana ndiponso dzuwa ndi mwezi. Musagwadire dzuwa kapena mwezi koma mugwadire Mulungu amene adazilenga izo ngati ndiye amene inu mumamupembedza
38.Koma ngati iwo ndi amwano palibe kanthu chifukwa pamaso pa Ambuye wako pali iwo amene amamulemekeza Iye usiku ndi usana ndipo satopa ayi
39.Ndipo pakati pa zizindikiro zake pali choti inu mumaona nthaka ili youma koma pamene Ife titumiza pa nthakayo madzi, iyo imakhala ndi moyo ndipo imakhala ndi zomera zambiri. Ndithudi, Iye amapereka moyo ku nthaka youma, ndithudi, akhoza kuperekanso moyo kwa anthu amene adafa. Ndithudi Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
40.Ndithudi onse amene sakhulupirira chivumbulutso chathu sadzatha kubisala. Kodi iye amene aponyedwa ku moto ndi wabwino kapena iye amene adzapulumutsidwa pa tsiku lachiweruzo? Chitani monga momwe mufunira. Ndithudi Iye amaona zonse zimene mumachita
41.Ndithudi iwo amene amakana uthenga pamene udza kwa iwo adzalangidwa. Ndithudi ili ndi Buku lolemekezeka kwambiri
42.Bodza silingalowemo kuchokera kumbali ina iliyonse. Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Mwini nzeru ndi olemekezeka
43.Palibe chimene chili kunenedwa kwa iwe kupatula chokhacho chimene chidanenedwa kwa Atumwi kale. Ndithudi Ambuye wako ndi Mwini kukhululukira ndiponso Mwini chilango chowawa
44.NdipoIfetikadatumizaBukulaKoranimuchiyankhulo china osati Chiarabu, iwo akadanena kuti, “Kodi bwanji mawu ake sali kufotokozeredwa bwinobwino? Chiyani! Chiyankhulo cha chilendo osati Chiarabu!” Nena, “Ilo ndi la iwo amene amakhulupirira, ndi chilangizo ndiponso mankhwala ochiritsa. Ndipo iwo amene sakhulupirira, makutu awo ndi ogontha ndipo ilo ndi khungu kwa iwo. Iwo ndiwo amene amaitanidwa kuchokera kutali.”
45.Ndithudi Ife tidamupatsa Mose Buku koma panabuka mikangano yotsutsana za ilo. Koma pakanapanda mawu amene adanenedwa kale ndi Ambuye wako, onse akadaweruzidwa kale. Ndithudi iwo amakayika kwambiri
46.Aliyense amene amachita zabwino amachitira moyo wake zabwino ndipo aliyense amene amachita zoipa amadzikundikira yekha mavuto. Ndithudi Ambuye wako sapondereza akapolo ake
47.Iye yekha ndiye amene amadziwa za ola. Ndipo palibe mtengo umene umabereka zipatso kapena chachikazi kuima kapena kubala popanda Iye kudziwa. Ndipo pa tsiku limene adzawafunsa onse kuti, “Kodi ali kuti amene munkati ndi anzanga?” Iwo adzayankha kuti, “Ife tili kunenetsa kwa Inu kuti palibe aliyense pakati pathu amene angachitire umboni.”
49.Munthu satopa akamapempha zinthu zabwino koma ngati mavuto adza pa iye, amataya mtima ndipo amakhala ndi nkhawa
50.Ndipo, ndithudi, Ife tikamuonetsera chifundo chathu atazunzika, ndithudi iye adzati: “Ichi ndi chifukwa cha nzeru zanga ndipo ine sindiganiza kuti ola lidzadza. Ndipo ngati ine ndibwerera kwa Ambuye wanga, ndithudi ine ndidzalandira zabwino kuchokera kwa Iye.” Ndithudi, Ife tidzawauza onse amene samakhulupirira zonse zimene adachita ndipo, ndithudi, Ife tidzawapatsa chilango chowawa kwambiri
51.Ndipo Ife tikamulangiza munthu chifundo chathu, iye amatembenuka ndi kuyamba kuchita zakezake koma ngati vuto lidza pa iye, amapemphera mosalekeza
52.Nena, “Ndiuzeni ngati ilo ndi lochokera kwa Mulungu ndipo inu muli kulikana. Kodi ndani amene angakhale wolakwa kwambiri kuposa iye amene amatsutsa mowirikiza?”
53.Ife tidzawaonetsa zizindikiro zathu za mlengalenga ndi za m’mizimu yawo, mpaka iwo atazindikira bwinobwino kuti ndi choonadi chenicheni. Kodi sizikwanira kuti Ambuye wanu ndiye mboni wa chinthu china chilichonse
54.Ndithudi! Tsopano iwo ali okayika pa zakukumana ndi Ambuye wawo. Ndithudi, ndiye amene wazungulira zinthu zonse