الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.oh inu anthu! Muopeni Ambuye wanu amene anakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo kuchokera kwa munthu ameneyu, Iye analenga mkazi wake. Ndipo kudzera mwa iwo, Iye adadzadza dziko lonse lapansi ndi anthu amuna ndi akazi osawerengeka. Opani Mulungu, dzina limene mumadandaulirana wina ndi mnzake. Ndipo lemekezani chibale. Ndithudi Mulungu amakuyang’anirani nthawi zonse
6.Aikeni ana a masiye pa mayesero mpakana pamene afika poti atha msinkhu. Ngati inu muona kuti ndi a maganizo okhazikika, apatseni chuma chawo ndipo musawaonongere iwo chuma chawo asanathe msinkhu. Munthu amene ali olemera asagwiritse ntchito katundu wa ana a masiye amene ali kumuyang’anira ndipo munthu osauka agwiritse ntchito chuma cha ana a masiye mosamala ndi mwa chilungamo. Pamene inu muwapatsa chuma chawo, itanani ena kuti akhale mboni; Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pa zonse zimene muchita
11.Mulungu wakulamulirani motere pankhani za ana anu: Mwana wa mwamuma adzalandira magawo awiri kuposa mwana wa mkazi. Ndipo ngati ana a akazi apitirira awiri, iwo adzalandira magawo awiri pa magawo atatu a katundu wosiyidwa koma ngati alipo mwana mmodzi yekha wamkazi, adzalandila theka ndipo makolo ake awiri, aliyense mwa iwo adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi – muzimene adasiya malemuyo ngati malemuyo ali ndi mwana. Koma ngati alibe mwana ndipo makolo ake ndiwo amene ayenera kulandira katundu wake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo atatu. Ngati iye ali ndi abale ake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi atatha kukwaniritsa lonjezo la malemu ndiponso kubweza ngongole. Inu simudziwa kuti pakati pa makolo anu ndi ana anu amene ali wa phindu ndi inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wanzeru ndi wodziwa chilichonse
12.Inu mudzalandira theka la chuma chimene akazi anu adasiya, ngati iwo alibe mwana. Ngati ali ndi mwana, inu mudzalandira gawo limodzi la magawo anayi la zimene mkaziyo wasiya pambuyo popereka zimene analonjeza ndi kubwezera ngongole. Nawo akazi anu adzapeza gawo limodzi m’magawo anayi muzimene mwasiya ngati mulibe mwana. Koma ngati muli ndi mwana, iwo, akaziwo, adzapeza gawo limodzi la magawo asanu ndi atatu a zimene mwasiya, pambuyo popereka zimene mudalonjeza ndi kubwezera ngongole. Ngati mwamuna kapena mkazi ndi yemwe wasiya katundu ndipo alibe mwana kapena mdzukulu, koma ali ndi mchimwene wake kapena mchemwali wake, aliyense wa iwo adzapeza gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi, ndipo ngati adali ambiri koposa apo adzagawana gawo limodzi la magawo atatu pambuyo popereka zimene analonjeza kapena kubwezera ngongole mosabweretsa mavuto. Limeneli ndi lamulo lochokera kwa Mulungu, Mulungu ndi wodziwa ndi woleza mtima
23.Inu mwaletsedwa kukwatira awa: Amayi anu, ana anu a akazi, alongo anu, azakhali anu, achemwali amayi anu, ana akazi achimwene anu, ana akazi a alongo anu, amayi amene adakuyamwitsani, akazi amene mudayamwitsidwa nawo bere limodzi, apongozi anu, ndi ana a akazi owapeza amene muli kuwasunga amene anabereka akazi amene mwawakwatira. Koma ngati simunagonepo ndi amai awo palibe choletsa kwa inu kuwakwatira atsikanawo. Kukwatiraakaziaanaanuamunaamenemudaberekainundi akazi awiri amimba imodzi nthawi imodzi ndi koletsedwa kupatula zimene zinachitika kale. Ndithudi Mulungu ndi okhululukira ndi wa chisoni chosatha
24.Ndipo ndikoletsedwa kukwatira akazi okwatiwa kupatula amene ali m’manja mwanu ngati akapolo. Limeneli ndi lamulo la Mulungu kwa inu. Ndipo ndi kololedwa kwa inu kukwatira wina aliyense amene sanatchulidwe pamwambapa ngati inu muwapatsa mphatso ya ukwati kuchokera ku chuma chanu mu njira yabwino osati ya chiwerewere. Amene muwakwatira , apatseni mphatso yawo ya ukwati motsatira malamulo. Koma pamene mphatso itchulidwa, sizolakwika kwa inu ngati mugwirizana. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa, ndi Waluntha
25.Ndipo ngati wina wa inu alibe mwayi woti nkukwatira mkazi wokhulupirira amene ndi mfulu, mukhoza kukwatira mwa atsikana anu wokhulupirira kuchokera kugulu la akapolo amene muli nawo, ndipo Mulungu amadziwa zonse za chikhulupiriro chanu ndipo inu ndinu amodzi. Akwatitseni ndi chilolezo cha ambuye awo ndipo muwapatse mphatso yawo ya ukwati mwa chilungamo. Iwo ayenera kudzisunga, osati a chiwerewere kapena wochita chibwenzi. Ndipo ngati akwatiwa ndipo achita chigololo, chilango chawo ndi theka la chilango chimene mfulu ya ikazi ingalandire. Ichi chikhudza iye amene aopa kupwetekeka pakati pa inu. Koma ndi kwabwino ngati inu mudziletsa ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
34.Anthu amuna ndi atetezi ndi osamala anthu akazi chifukwa Mulungu wawalemekeza ena kuposa anzawo ndiponso chifukwa cha chuma chawo chimene amagwiritsa ntchito. Motero akazi ochita zabwino ndipo amene amamvera, amasunga pamene amuna awo palibe, ndi zimene Mulungu awalamulira kuti azisunge. Ndipo akazi amene mukuona kuti samvera achenjezeni ndipo ngati iwo sasintha asiyeni agone pa okha ndipo ngati sasinthabe amenyeni. Koma ngati iwo akumverani, musawafunire njira yachabe. Ndithudi Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu
77.Kodi siunaone anthu amene amauzidwa kuti: “Musamenye nkhondo, pempherani mwandondomeko ndipo perekani msonkho wothandizira anthu osauka,” koma pamene iwo adalamulidwa kuti amenye nkhondo, taona; enaaiwoamaopaanthumongamomweamamuopera Mulungu kapenanso kuposa apa. Iwo amati: “Ambuye wathu! Kodi ndi chifukwa chiyani mwatilamula kuti timenye nkhondo? Kodi simungatipatse nthawi yopumula ngakhale yochepa” Nena: “Chisangalalo cha moyo uno ndi chochepa kwambiri. Moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwambiri kwa iye amene amaopa Mulungu ndipo inu simudzaponderezedwa ndi pang’onong’ono pomwe.”
92.Ndi chinthu choletsedwa kuti munthu wokhulupirira aphe mzake wokhulupirira kupatula mwangozi. Ndipo aliyense amene, mwangozi, akupha munthu wokhulupirira ayenera kumasula kapolo wokhulupirira m’modzi ndi kulipira ndalama zopepesera ku banja la ophedwayo, kupatula ngati iwo asankha kuti amukhululukira munthu wakuphayo. Ngati malemuyo anali wochokera kwa adani anu ndipo anali wokhulupirira, chilango chake ndi kumasula kapolo m’modzi wa wokhulupirira. Koma ngati malemuyo anali ochokera ku mtundu wa athu ogwirizana nawo, ndalama za chipepeso ziyenera kuperekedwa kubanja la munthu wakufayo ndi kumasula kapolo mmodzi wa wokhulupirira. Ngati munthu sangathe kupeza izi, ayenera kusala miyezi iwiri motsatizana ndi cholinga chopeza chikhululukiro kwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi Wodziwa ndi Waluntha
102.Pamene iwe uli pakati pawo ndipo uli kuwatsogolera pa mapemphero, lola gulu lina la iwo kuti liime pamodzi ndi iwe, atanyamula zida zawo za nkhondo. Akatha kugwetsa nkhope zawo pansi apite kumbuyo kwanu ndipo libwere gulu lina limene silinapemphere kuti lipemphere nawe, ayenera kukhala tcheru ndi kutenga zida zawo za nkhondo. Anthu osakhulupirira amafuna inu mutaiwala zida zanu ndi katundu wanu kuti akukantheni nthawi imodzi, koma palibe cholakwa ngati musiya zida zanu chifukwa cha mavuto ena monga mvula kapena matenda koma khala tcheru. Ndithudi Mulungu wawakonzera anthu wosakhulupirira chilango chochititsa manyazi
171.oh inu anthu a m’Buku! Musadutse malire a chipembedzo chanu kapena kunena zokhudza Mulungu kupatula choonadi. Messiya Yesu, mwana wa Maria, sadali wina aliyense koma Mtumwi wa Mulungu ndi Mawu ake amene adanena kwa Maria, ndi Mzimu wolengedwa ndi Iye. Kotero khulupirirani mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Ndipo musanene kuti: “Atatu.” Siyani! Zidzakhala bwino kwa inu. Chifukwa Mulungu ndi mmodzi yekha. Ulemerero ukhale kwa Iye. Iye sangakhale ndi mwana. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi wodalirika
176.Iwo amakufunsa za malamulo; Nena: “Mulungu akukuuzani za munthu amene alibe makolo kapena mwana. Ngati munthu wa mwamuna akufa, ndipo alibe mwana koma ali ndi mlongo wake, mlongo wake adzalandire theka la katundu amene asiya. Ndipo ngati mkazi sasiya mwana, mlongo wake adzatenga chuma chake. Koma ngati akhala ndi alongo ake awiri, iwo adzalandire magawo awiri a magawo atatu a katundu amene asiya. Ndipo ngati pali abale amuna ndi akazi, mwamuna adzalandira magawo amene angalandire akazi awiri. Mulungu akukulongosolerani kuti musasochere. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse.”