3.Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga iwo asanadze ndipo iyo idalira poona kuti padalibe nthawi yothawa
4.Ndipo iwo ali kudabwa kuti Mtumwi wadza kwa iwo kuchokera pakati pawo. Ndipo anthu osakhulupirira amati, “Uyu ndi munthu wamatsenga ndiponso wabodza!”
6.Ndipo atsogoleri awo amachoka monyinyirika nati, “Pitirizani inu ndipo mudzipereke kwathunthu kwa milungu yanu! Ndithudi ichi ndi chinthu choti chikusokonezani.”
8.“Kodi uthenga wavumbulutsidwa kwa iye yekha pakati pathu?” Iyayi! Koma iwo ali kukayika za uthenga wanga. Iyayi! Iwo sadalawepo chilango changa
9.Kapena iwo ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wako, Mwini Mphamvu zonse, Mwini kupereka zabwino zonse
10.Kapena iwo ali ndi ulamuliro kumwamba ndi padziko ndi kuti zonse zimene zili m’menemo ndi zawo? Ngati nditero, alekeni iwo kuti akwere mothandizidwa
12.Asanadze iwo, panali ena amene adakana Atumwi. Anthu a Nowa, a Aad, ndi a Farawo, mfumu ya zisonga
14.Panalibe mmodzi amene sadanene kuti Atumwi adali abodza, motero chilango changa chinali chowayenera
16.Iwo amati, “Ambuye wathu, bweretsani msanga kwa ife Buku la ntchito zathu ngakhale nthawi yake siinakwane.”
17.Khala wopirira pa zimene ali kunena ndipo uzikumbukira kapolo wathu Davide, munthu wamphamvu. Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse
18.Ndithudi Ife tidauza mapiri kuti aziyimba pamodzi ndi iye mayamiko athu nthawi ya madzulo ndi m’mbandakucha
20.Tidalimbikitsa Ufumu wake ndipo tidamupatsa nzeru ndi kuweruza kwabwino m’manenedwe ndi m’chiweruzo
21.Kodi nkhani ya anthu okangana yakupeza iwe? Pamene, iwo adakwera chipupa cha nyumba ndi kulowa mnyumba ya padera
22.Pamene adalowa kwa Davide, iye adachita mantha ndi iwo ndipo iwo adati, “Usaope. Ife ndife anthu okangana, ndipo wina wa ife wachimwira mnzake motero weruza mwachilungamo ndipo usatiweruze opanda chilungamo koma titsogolere ku njira yoyenera.”
23.“Ndithudi uyu ndi m’bale wanga ndipo ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi pamene ine ndili ndi nkhosa imodzi yokha basi. Komabe iye akuti, ‘Undipatse ine nkhosayo’ ndipo iye adandipambana mu zonena zake.”
24.Iye adati, “Ndithudi iye wakulakwira kwambiri pokupempha kuti nkhosa yako imodzi yokha iperekedwe kwa iye kuonjezera pa zimene ali nazo.” Ndithudi anthu ambiri ochitira pamodzi malonda ndi amene akulakwirana wina ndi mnzake. Koma izi sizichitika ndi anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndipo anthu otere ndi ochepa. Ndipo Davide adazindikira kuti Ife tidamuyesa iye ndipo adapempha chikhululukiro kwa Ambuye wake ndipo iye adagwa nagunditsa mphumi yake pansi ndi kudza molapa
25.Kotero Ife tidamukhululukira ndipo ndithudi adali kufupi ndi Ife ndipo ali ndi malo okongola pa nthawi yobwerera
26.Iwe Davide! Ndithudi Ife takukhazika iwe kukhala Kazembe padziko lapansi motero weruza pakati pa anthu mwachilungamo, ndipo usatsatire zilakolako za mtima wako chifukwa zidzakusocheretsa ku njira ya Mulungu. Ndithudi iwo amene asochera ku njira ya Mulungu adzalangidwa kwambiri chifukwa iwo amaiwala za tsiku lachiweruzo
27.Si kuti tidasowa chochita polenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’kati mwake! Amenewo adali maganizo a anthu osakhulupirira! Ndipo tsoka kwa anthu osakhulupirira lochokera ku moto
28.Kodi Ife tingasamale mofanana anthu okhulupirira ndi ochita ntchito zabwino ndi iwo amene amadzetsa chisokonezo pa dziko? Kapena Ife tingasamalire anthu amene amalewa zoipa chimodzimodzi ndi iwo amene amachita zoipa
29.Ili ndi Buku limene Ife tatumiza kwa iwe, lodzala ndi madalitso kuti akhoza kuganiza mofatsa pa mavesi ake ndi kuti anthu ozindikira akhoza kukumbukira
31.Ndipo pamene adadza nazo kwa iye, nthawi ya madzulo, Hatchi zophunzitsidwa bwino zamphamvu ndi zoberekedwa bwino
32.Ndipo iye adati, “Ndithudi ine ndidakonda chuma kuposa kukumbukira Ambuye wanga. Mpaka pamene nthawi idatha ndipo dzuwa lidalowa mu mdima.”
33.Ndipo iye adati “Bweretsani mahatchi kwa ine.” Ndipo iye adayamba kuzisisita miyendo ndi makosi awo
34.Ndipo, ndithudi, Ife tidamuyesa Solomoni ndipo Ife tidaika Satana pa mpando wake wachifumu koma iye adadza kwa Ife modzipereka ndi molapa
35.Iye adati, “Ambuye wanga! Khululukireni ndipo ndipatseni ufumu umene simudzapatsanso wina pambuyo panga chifukwa inu mumapereka zokoma zanu mopanda muyeso.”
36.Ndipo Ife tidamuchepetsera mphamvu yakuti mphepo imvere malamulo ake kuti iziyenda potsatira malamulo ake amene iye adalamula
37.Ndiponso a Satana ochokera kwa majini ndi m’misiri aliyense womanga nyumba ndi wodziwa kusambira pa madzi
39.Iyi ndi mphatso yathu yaulere, kotero pereka mowolowa manja kapena kuisunga. Iwe siudzaimbidwa mlandu
41.Ndipo kumbukira kapolo wathu Yobu pamene adapempha kwa Ambuye wake kuti, “Satana wandikundikira mavuto ndi masautso.”
43.Ndipo Ife tidamubwezera banja lake ndi kuonjezera chiwerengero chawo ngati chisomo chochokera kwa Ife ndiponso chikumbutso kwa anthu ozindikira
44.Ndipo nyamula m’manja mwako mtolo wa udzu ochepa ndipo mumenye nawo koma usaphwanye lonjezo lako. Ndithudi! Ife tidamupeza ali wopirira kwambiri ndi okhazikika. Ndithudi iye adali Mtumwi wabwino! Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse
45.Ndipo kumbukira akapolo athu Abrahamu, Isake, Yakobo ameneadaliodzalandimphamvundiponsoomvetsa zinthu za chipembedzo
51.M’menemo iwo adzakhala mwamtendere ndiponso m’menemo iwo adzaitanitsa zipatso zochuluka ndi zakumwa zokoma
59.Ili ndi gulu la nkhondo limene lili kulowa ndi inu! Palibe kulandiridwa kwabwino kwa iwo! Ndithudi iwo adzalowa kumoto
60.Iwo adzati, “Iyayi! Inunso. Simulandiridwa ayi. Ndinu amene mudatinyenga ife, kotero awa ndiwo malo oipa kwambiri kukhalako.”
61.Iwo adzati, “Ambuye wathu! Aliyense amene adachititsa kuti zimenezi zidze kwa ife muonjezereni kawiri chilango chake cha kumoto.”
62.Ndipo iwo adzati, “Kodi zachitika bwanji kuti ife sitili kuona anthu amene tinkawawerenga pakati pa anthu ochita choipa?”
65.Nena, “Ndithudi ine ndine mchenjezi basi ndipo kulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha, wopambama ndi wofunika.”
66.“Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo. Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wokhululukira nthawi zonse.”
75.Mulungu adati, “Iwe Satana! Chakuletsa ndi chiyani kulambira munthu amene ndalenga ndi manja anga? Kodi ndiwe wamwano? Kodi kapena iwe ndiwe mmodzi wa apamwamba?”
76.Iye adati, “Ine ndine wopambana kuposa iye. Inu mudandilenga ine kuchokera kumoto pamene iye mudamulenga kuchokera ku dothi.”