5.Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi wa zonse zimene zili m’menemo ndi Ambuye wa dera lililonse lotulukira dzuwa
8.Kotero iwo sangathe kumvetsera zokambidwa za gulu lapamwamba chifukwa iwo amapirikitsidwa kuchokera kumbali iliyonse
10.Kupatula yekhayo amene amakwatula zinthu mwakuba, ndipo amathamangitsidwa ndi moto woyaka ndi wowala kwambiri
11.Ndipo tawafunsa, “Kodi iwo ndi a mphamvu kuposa zolengedwa zina zimene tidalenga?” Iwo tidawalenga kuchokera ku dothi lonyata la makande
22.(Kudzanenedwa kuti); “Bweretsani anthu ochimwa pamodzi ndi anzawo ndi zinthu zimene iwo anali kupembedza.”
35.Ndithudi pamene iwo, adauzidwa kuti, “Kulibe mulungu wina koma Mulungu weniweni, iwo anali kudzitukumula.”
85.Pamene iye adati kwa atate wake ndi anthu a mtundu wake, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?”
102.Ndipo pamene iye adakula mofika pa msinkhu woti angathe kuthandiza abambo ake, iye adati: “Mwana wanga! Ndithudi ine ndalota ndili kukupha ngati nsembe. Taganiza zimene uli kuziona.” Iye adati, “Atate wanga! Inu chitani monga momwe mwalamulidwira. Ngati Mulungu afuna, mudzandipeza ine wopirira!”
105.“Ndithudi wakwaniritsa maloto ako.” Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita zabwino
113.Ndipo Ife tidaika madalitso athu pa iye ndi pa Isake. Ndipo pakati pa ana awo pali ena ochita ntchito zabwino ndi ena amene ndi olakwa ndipo amadzipondereza okha
158.Ndipo iwo akhazikitsa ubale pakati pa Mulungu ndi majini. Koma majini amadziwa kuti iwo adzatengedwa kupita kwa Iye
180.Ulemerero ukhale kwa Ambuye wako, Ambuye wolemekezeka ndi wamphamvu, kuposa zimene ali kumukundikira