11.Ukhoza kumuchenjeza yekhayo amene watsatira chikumbutso ndi kuopa Mwini Chisoni ngakhale kuti iye sangamuone. Kwa iye umuuze nkhani yabwino ya chikhululukiro ndi mphotho yopambana
12.Ndife amene tidzadzutsa anthu akufa ndi kulemba ntchito zonse za anthu ndi zizindikiro zimene asiya m’mbuyo: Talemba zonse mooneka bwino kwambiri m’buku
14.Pamene Ife tidawatumizira iwo awiri, iwo adawakana. Motero Ife tidatumizanso wina wachitatu, ndipo iwo adati, “Ndithudi ife tatumizidwa kwa inu.”
15.Iwo adati, “Inu ndinu anthu ngati ife tomwe. Mwini chisoni sadavumbulutse china chilichonse! Inu muli kunama basi.”
18.Anthu adati, “Tili kuona malodza. Ngati mupitiriza tikuponyani miyala ndipo chilango chowawa chizadza pa inu.”
19.Iwo adati, “Malodza anu akhale ndi inu! Kodi chifukwa chakuti mwachenjezedwa? Iyayi koma inu ndinu anthu ochimwa kwambiri
20.Nthawi yomweyo munthu wina adadza ali kuthamanga kuchokera kumbali ina ya mzinda. Iye adati, “Anthu anga! Tsatirani iwo amene atumidwa ndi Mulungu.”
21.“Atsatireni iwo amene safuna malipiro kuchokera kwa inu pokukumbutsani mawu a Mulungu ndipo ndi otsogozedwa bwino.”
22.“Kodi pali chifukwa chotani chimene chingandilepheretse ine kuti ndim’pembedze Iye amene adandilenga popeza ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera?”
23.“Kodi ine ndizipembedza milungu ina osati Iyeyo? Ngati ndi chifuniro cha Mwini chisoni kundizunza, kukhala pakati kwawo sikudzandithandiza ndipo iwo sadzandipulumutsa ayi.”
26.Kudanenedwa kwa iye kuti, “Lowa mu Paradiso.” Iye adafuula kuti, “Akadakhala kuti anthu anga adadziwa.”
28.Ndipo Ife sitidatumize padziko lapansi, kwa anthu ake, gulu lochokera kumwamba kuti lilimbane nawo ndipo sikudali koyenera kuti Ife tichite choncho
31.Kodi iwo sadaone mibadwo yakale imene tidaiononga zaka zikwizikwi iwo asanabadwe? Ndipo iwo sadzabwereranso
33.Chizindikiro kwa iwo ndi nthaka yakufa imene tidaidzutsa ndipo timatulutsa m’nthakamo nthangala zomwe iwo amadya
36.Ulemerero ukhale kwa Iye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi) zimene zimamera m’nthaka ndi zina za mtundu wawo ndi zinanso zimene sazidziwa
38.Dzuwa limayenda mofulumira kupita kumalo ake okapuma. Umenewu ndiwo ulamuliro wa Mwini Mphamvu zonse ndiponso Wodziwa chilichonse
39.Ndipo mwezi tidaulamulira kuti uyende mumsewu wake mpaka pamene ukamabwerera ngati nthawi yoyamba m’maonekedwe
40.Dzuwa sililoledwa kupitirira mwezi ndipo usiku siupyola usana. Chilichonse chimayenda mumsewu wake
45.Pamene zinenedwa kwa iwo kuti, “Opani chinthu chimene chili patsogolo panu ndi pambuyo panu kuti mwina Mulungu angakuonetsereni chifundo” ndipo iwo samvera ayi
46.Ndithudi palibe chizindikiro chochokera kwa Ambuye wawo chimene iwo amachivomera. Ndipo iwo salabadira
47.Ndipo pamene auzidwa kuti, “Perekani gawo la chopereka chaulere pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani.” Anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ife tizidyetsa iwo amene Mulungu atafuna akhoza kuwadyetsa? Ndithudi inu ndi osochera kwambiri.”
48.Iwo amanenanso kuti, “Kodi lonjezo limeneli la tsiku lachiweruzo lidzatsimikizidwa liti, ngati zimene uli kunenazi ndi zoona?”
52.“Tsoka kwa ife!” Iwo adzatero. “Ndani amene watidzutsa kuchokera kumalo athu a mpumulo?” Ichi ndi chimene Ambuye wachifundo adalonjeza. “Atumwi adanenadi zoona!”
54.Patsiku limeneli sipadzakhala mzimu umene siudzaweruzidwa ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu
60.“Kodi Ine sindidakuchenjezeni, inu ana a Adamu, kuti musamagwadire Satana, chifukwa iyeyu ndi mdani wanu woonekeratu?”
65.Lero, Ife titseka pakamwa pawo, ndipo manja awo ndi amene ayankhule ndi Ife ndiponso miyendo yawo ichitira umboni pa ntchito zoipa zimene anali kuchita
66.Chikadakhala cholinga chathu, tikadawachititsa khungu kuti azivutika poyenda. Nanga akadaona bwanji machimo awo
67.Chikadakhala cholinga chathu, tikadawasintha kuti asanduke china chake pamalo pamene adaimirira, kuti asapite patsogolo kapena kubwerera m’mbuyo
69.Ife sitidamuphunzitse iye ndakatulo ayi ndiponso si koyenera kuti akhale mlakatuli. Ichi si china koma chikumbutso ndi dongosolo la Korani
71.Kodi iwo saona kuti pakati pa zinthu zimene tidalenga ndi manja athu tidawalengera nyama zimene iwo amazilamulira
74.Iwo akhazikitsa milungu ina powonjezera pa Mulungu weniweni, poganiza kuti mwina akhoza kuthandizidwa
76.Usalole kuti mawu awo akumvetse chisoni. Ife tikudziwa zonse zimene azibisa ndi zonse zimene akuzionetsa
77.Kodi munthu, sadziwa kuti tidamulenga kuchokera ku dontho la umuna? Koma iye ndi otsutsana ndi Ife poyera
78.Iye amatifanizira Ife ndi zina zake ndipo amaiwala za chilengedwe chake. Iye amafunsa kuti, “Kodi ndani amene adzapereka moyo ku mafupa oola?”
79.Nena “Iye amene adawalenga poyamba adzawapatsa moyo. Iye amadziwa chilichonse cha zolengedwa zake.”
81.Kodi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, alibe mphamvu zolenga china chake chofanana nazo? Ndithudi ali nazo. Iye ndi Mlengi amene amadziwa chinthu china chilichonse
83.Ulemerero ukhale kwa Iye amene ali ndi ulamuliro pa chinthu china chilichonse; ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera