2.Ichi ndi chivumbulutso cha Buku Lopatulika limene mulibe zokayikitsa ndi chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse
3.Kodi kapena iwo amati wapeka yekha? Iyayi, ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wake kuti uchenjeze anthu amene kuyambira kale mchenjezi sanadze kwa iwo, kuti iwo akhoza kutsatira njira yoyenera
4.Mulungu ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko Sajda 439 lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero Iye adabuka pa mpando wake wachifumu. Inu mulibe wokuyang’anirani kapena wokuthandizani kupatula Iye yekha. Kodi simungaganize
5.Iye amalamulira zinthu kuchokera kumwamba mpaka pa dziko lapansi ndipo zidzakwera kudza kwa Iye m’tsiku limene muyeso wake ungathe kuyerekezedwa ndi zaka chikwi chimodzi mwa chiwerengero chomwe inu mumachidziwa
9.Ndipo iye adamuumba munthu mwaubwino ndipo adamuuzira Mzimu wake. Ndipo Iye adakupatsani inu makutu, maso ndi mitima, inu simuthokoza nthawi zambiri
10.Iwo adati, “Chiyani! Pamene ife taikidwa m’manda, kodi tingadzalengedwenso?” Ndithudi iwo adakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo
11.Nena “Mngelo wa imfa, amene adasankhidwa kukuyang’anirani inu, adzakupangitsani kuti mufe. Kotero inu mudzabwerera kwa Ambuye wanu.”
12.Iwe ukadangodzaona mmene anthu ochimwa adzagwetsera mitu yawo pamaso pa Ambuye wawo nati, “Ambuye wathu! Ife taona ndipo tamva. Tsopano tibwezereni pa dziko lapansi ndipo ife tidzagwira ntchito zachilungamo chifukwa ife, ndithudi, takhulupirira.”
13.Ife tikadafuna, ndithudi, tikadatsogolera mzimu uliwonse ku njira yoyenera. Koma kuti mawu ochokera kwa Ine adakwanitsidwa. “Ine ndidzadzadza Gahena ndi majini pamodzi ndi anthu.”
14.Lawani chilango tsopano, chifukwa inu mudaiwala za tsikuli. Ndipo nafenso takuiwalani. Kotero inu lawani chilango chosatha chifukwa cha ntchito zanu zoipa
15.Ndi okhawo amene amakhulupirira chiphunzitso chathu amene chiphunzitsocho chimati chikaphunzitsidwa, amagwa pansi kupembedza ndipo amayamikandikulemekeza Mulunguwawomodzichepetsa
16.Iwo amasiya makama awo ndi cholinga chopempha kwa Ambuye wawo mwamantha ndi mwa chikhulupiriro. Ndipo amapereka zaulere kuchokera ku chuma chimene tidawapatsa
17.Tsopano palibe munthu amene amadziwa madalitso amene ali kuwasungira m’nkhokwe ngati malipiro a ntchito zawo zabwino
19.Iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalandira minda ngati malo awo okhala chifukwa cha ntchito zawo zabwino zimene anachita
20.Ndipo iwo amene amaswa malamulo, malo awo okhala ndi kumoto ndipo nthawi zonse zimene iwo adzafuna kuchokako, adzabwezedwanso komweko. Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Lawani ululu wa moto umene munkati ndi bodza.”
21.Ndipo, ndithudi, Ife tidzawalawitsa, chilango cha m’moyo uno chisanadze, chilango choyamba kuti mwina akhoza kutembenuka
22.Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amati akakumbutsidwa chiphunzitso cha Ambuye wake, iye amabwerera m’mbuyo? Ndithudi Ife tidzalanga anthu ochimwa
23.Ndipo, ndithudi, Ife tidamupatsa Buku Mose ndipo musakayike za kulandira kwake ndipo tidalipanga ilo kukhala chotsogolera ana a Israyeli
24.Ndipo tidasankha pakati pawo, atsogoleri amene amapereka malangizo potsatira malamulo athu, pamene iwo anali kupirira ndi kukhulupirira mu chiphunzitso chathu
25.Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku louka kwa akufa pa nkhani zimene anali kutsutsana
26.Kodi icho sichiwaphunzitsa phunziro kuti kodi ndi mibadwo ingati imene tidaononga iwo asanadze, m’nyumba zawo zimene amalowa ndi kutulukamo? Ndithudi mu izo muli chiphunzitso. Kodi iwo sangamve
27.Kodi iwo saona kuti Ife timagwetsa mvula panthaka youma ndi kumeretsa mbewu zimene iwo ndi ziweto zawo zimadya? Kodi alibe maso oti angaone
29.Nena, “Pa tsiku lachiweruzo, chikhulupiriro cha iwo amene sakhulupirira sichidzawathandiza ndiponso sadzapeza mpumulo.”