الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Alif Lam Mim
7.Ndiye amene wavumbulutsa kwa iwe Buku. Ndipo ena mwamavesiakealindimatanthauzoozindikirika, omwendi mazikoa Buku, pameneenandiovutakuwazindikira. Ndipo iwo amene mitima yawo yadzazidwa ndi chisokonekero, iwo amatsatira mavesi amene ndi ovuta kuwazindikira ndi cholinga chofuna chisokonezo ndi kufuna kupereka matanthauzo awoawo. Koma palibe amene amadziwa matanthauzo ake kupatula Mulungu. Ndipo iwo amene ali ndi nzeru amati: “Ife timakhulupirira mwa ilo chifukwa lonse ndi lochokera kwa Ambuye wathu.” Ndipo palibe amene amalabadira kupatula okhawo amene ali ndi nzeru
49.Ndipo adzamupanga iye kukhala Mtumwi wa ana a Israyeli nati: “Ine ndadza kwa inu ndi chizindikiro chochokera kwa Ambuye wanu ndipo kuchokera ku dothi ndidzakuumbirani chinthu chofanana ndi mbalame ndipo ine ndidzaipumira mpweya ndipo ndi chilolezo cha Mulungu idzakhala mbalame ya moyo. Ndi chilolezo cha Mulungu, ine ndidzachiza anthu a khungu, akhate ndi kuukitsa anthu akufa. Ine ndidzakuuzani zimene muzidya ndi zimene musunga m’nyumba mwanu. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati muli okhulupirira.”
73.Ndipo musakhulupilire wina aliyense kupatula amene atsatira chipembedzo chanu. Nena: “Ndithudi! Chilangizo choonadi ndi chilangizo cha Mulungu” ndipo musakhulupirire kuti wina wake adzapatsidwa chinthu cholingana ndi chimene chapatsidwa kwa inu. Kapena iye adzatsutsana nanu pamaso pa Ambuye wanu. Nena: “Ndithudi zonse zili m’manja mwa Mulungu. Iye amazipereka kwa aliyense amene Iye wamufuna. Ndipo Mulungu ali ndi chili chonse chimene zolengedwa zake zimafuna, Mwini kudziwa chilichonse.”
154.Ndipo chitantha chisoni, adakutsitsirani mtendere kuti udze pa inu. Ndipo tulo tidagwira ena a inu pamene ena adangogona kumavutika m’maganizo, chifukwa cha zilakolako zawo, kuganiza mosalungama ndikukhala ndi maganizo a umbuli okhudza Mulungu. Iwo adafunsa: “Kodi ife tili ndi chonena pankhani iyi?” Nena: “Zonse zili m’manja mwa Mulungu.” Iwo amabisa m’mitima mwawo zinthu zimene safuna kuulula kwa iwe. Iwo amanena kuti: “Tikadakhala kuti tidaloledwa kunenapo maganizo athu pankhaniyi, ife sitikanaphedwa pano.” Nena: “Ngakhale inu mukadakhala kunyumba zanu ndithudi ena amene adalembedwa kuti aphedwe akadapita ku malo kumene akadakaphedwa.” Ndipo Mulungu adachita zimenezi kuti ayese zimene zili m’mitima mwanu ndi kuyeretsa zimene zili m’mitima mwanu ndipo ndithudi Mulungu akudziwa zimene zili m’mitima
195.Motero Ambuye wawo adavomera pemphero lawo nati: “Ine sindidzaononga mphoto ya ntchito za munthu wa mwamuna kapena wa mkazi amene ali pakati panu.” Inu ndinu amodzi. Iwo amene adasamuka m’nyumba zawo ndi kupirikitsidwa kuchoka mu izo ndi kuzunzidwa mu njira yanga ndi iwo amene adamenya nkhondo ndi kuphedwa mnjira yanga, ndithudi, Ine ndidzawakhululukira machimo awo ndipo ndidzawalowetsa ku minda yothiriridwa ndi madzi a m’mitsinje yoyenda pansi pake, mphatso yochokera kwa Mulungu. Ndipo kwa Mulungu ndiye kumene kuli malipiro abwino