الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Ife tavumbulutsa mutu uwu ndipo taupanga kukhala wokakamiza ndipo ndi mwa iwo mmene tavumbulutsa chivumbulutsochoonekakutiinumukhozakuchenjezedwa
31.Auze akazi okhulupirira kuti azitsitsa maso awo ndipo asachite chiwerewere ndiponso azibisa zinthu zimene zimawakongoletsa kupatula zokhazo zimene sizingabisike. Ndipo azifunda nsalu kumutu ndi pa chifuwa chawo ndiponso asaonetse kukongola kwawo kupatula kwa amuna awo, abambo awo, abambo a amuna awo, ana awo aamuna, ana a amuna awo, ana a chemwali awo kapena ana a achimwene awo kapena ana a alongo awo kapena akazi anzawo owakhulupirira; ndiponso antchito awo aakazi, a ntchito awo a amuna ndi ana amene alibe chilakolako cha akazi. Ndipo iwo asamamenyetse mapazi awo pansi akamayenda ndi cholinga choonetsa zina zokongola zawo zobisika. Oh inu okhulupirira! Lapani kwa Mulungu mogonja kuti mupambane
33.onse amene sangathe kukwatira adzisunge mpaka pamene Mulungu awapatsa iwo zabwino zake. Akakhala a kapolo anu amene afuna kugula ufulu wawo, amasuleni ngati inu muona kuti iwo ndi abwino ndipo muwapatseko gawo la chuma chimene Mulungu wakupatsani inu. Inu musadzakakamize akapolo anu aakazi kuti azichita chiwerewere ngati iwo afuna kudzisunga ndi cholinga chofuna kupeza zinthu zabwino za padziko lapansi. Ngati wina aliyense awakakamiza iwo, Mulungu adzawakhululukira ndi kuonetsa chisoni chake pa iwo
35.Mulungu ndi Muuni wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kuunika kwake kukhoza kufaniziridwa ndi malo olowa m’chipupa amene m’kati mwake muli nyali imene ili m’galasi looneka ngati nyenyezi yowala. Iyo imayatsidwa kuchokera ku mtengo wodalitsika wa Azitona umene siuli kum’mawa kapena kumadzulo. Mafuta ake amatha kuwala ngakhale kuti palibe moto owayakitsa mafutawo. Muuni pa Muuni unzake ndipo Mulungu amatsogolera, ndi kuwala kwake, aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu amapereka zitsanzo kwa anthu. Ndipo Mulungu amadziwa chilichonse
58.oh inu anthu okhulupirira! Lolani akapolo anu aamuna ndi aakazi ndi ana amene sanathe msinkhu kuti apemphe poyamba pa nthawi zitatu, musadapemphere pemphero la m’mawa kapena pamene mwavula zovala zanu masana chifukwa cha kutentha kapena mutatha kupemphera mapemphero a usiku. Izi ndi nthawi zitatu zokhala panokha. Palibe chifukwa kwa inu kapena kwa iwo kuchezerana, wina ndi mnzake mu nthawi zina kupatula nthawi zimene zatchulidwazi. Kotero Mulungu amaulula poyera chivumbulutso chake kwa inu. Ndipo Mulungu ndi Wodziwa ndi Waluntha
61.Si cholakwa ngati munthu wakhungu kapena wolumala kapena wodwala kapena inu eni ake mudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu kapena m’nyumba za amayi anu kapena m’nyumba za achimwene anu kapena m’nyumba za alongo anu kapena m’nyumba za achimwene a atate anu kapena alongo awo atate anu kapena m’nyumba za amalume anu kapena m’nyumba za achemwali a amayi anu kapena m’nyumba zimene makiyi ake mwasunga kapena aliyense m’nyumba za abwenzi anu. Palibe cholakwa kwa inu ngati mudya pamodzi kapena payekha payekha. Pamene mulowa m’nyumba, lonjeranani wina ndi mnzake malonje odalitsika ochokera kwa Mulungu. Kotero Mulungu ali kukufotokozerani zizindikiro kuti mukhoza kukhala ozindikira
62.Ndi okhawo amene ali ndi chikhulupiriro, amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amati akasonkhana pamodzi ndi iye pa zinthu zofunika sachoka mpaka pamene apempha chilolezo chake. Ndithudi anthu amene amakupempha chilolezo ndiwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Pamene akupempha iwe chilolezo choti achoke ndi cholinga chokagwira ntchito zawo, pereka chilolezo kwa aliyense amene iwe wamufuna ndipo mumupemphe Mulungu kuti awakhululukire machimo awo. Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha