الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.oh anthu inu! opani Ambuye wanu ndipo kwaniritsani udindo wanu kwa Iye. Ndithudi chivomezi cha nthawiyo chidzakhala choopsa kwambiri
5.Oh anthu inu! Ngati inu mukayika za kuukanso kwa akufa, ndithudi, Ife tidakulengani kuchokera ku dothi, ndi kudontho la umuna, losakanizana ndi ukazi ndiponso kuchokera ku mnofu oumbidwa bwino osonyeza ziwalo za munthu ndi wina mnopfu umene siunayambe kusonyeza ziwalo kuti tikusonyezeni mphamvu zathu. Ndipo Ife timakhazikitsa m’chiberekero cha mkazi chilichonse chimene tifuna panthawi yomwe yaikidwa ndipo timakutulutsani ngati makanda ndipo mumakula kufika pa msinkhu waumunthu. Ndipo ena a inu amafa ndipo ena amabwezeredwa moyo wapansi kuti asadziwe zonse zimene anali kudziwa kale. Ndipo inu mumaona nthaka ili youma yosamera chilichonse koma tikatsitsa madzi panthakapo, iyo imayamba kugwedezeka ndi kutupa ndi kumeretsa mbewu zokongola zamitundumitundu
78.Ndipo limbikani kwambiri chifukwa cha chipembedzo chaMulungumongammenezikufunikira.Iyewakusankhani inu ndipo sadakukundikireni mavuto muchipembedzo chanu. Chipembedzo cha Abrahamu atate wanu. Iye ndiye amene akupatsani inu dzina lakuti Asilamu kuyambira kalekale ndiponso mu dzinali Mtumwi ndiye mboni yanu, ndipo nanunso mukhale mboni ya anthu anzanu. Pitirizani mapemphero, perekani msonkho wothandizira anthu osauka ndipo khulupirirani mwa Mulungu. Iye ndi Mtetezi wanu wabwino ndiponso Mthandizi wabwino kwambiri