2.Palibe chenjezo limene limadza kuchokera kwa Ambuye wawo limene iwo amalimvera kupatula pamene iwo ali kusewera
3.Ndi mitima yotangwanika, iwo amene amachita zoipa amauzana mwamseri kuti, “Kodi uyu si munthu ngati inu? Kodi inu mukutsatira matsenga pamene muli kuona?”
4.Iye adati: “Ambuye wanga amadziwa chilichonse chimene chimanenedwa kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amamva zonse ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.”
5.Koma ena amati, “Ichi si china koma maloto a bodza! Iyayi! Iye walipeka. Iyayi, iye ndi mlakatuli! Ndipo mulekeni atilangize ife chizindikiro china monga momwe Atumwi akale ankachitira.”
6.Palibe umodzi wa mizinda imene tidaononga imene idakhulupirira iwo asanadze. Kodi iwo adzakhulupirira
7.Ndipo Ife, iwe usadabwere sitidatumize ena, koma amuna omwe timawapatsa chivumbulutso. Motero afunse anthu ozindikira ngati iwe siudziwa
9.Ndipo Ife tidakwaniritsa lonjezo lathu kwa iwo, ndipo tidawapulumutsa iwo pamodzi ndi ena amene Ife tidawafuna koma tidaonongeratu anthu onse ochimwa
11.Kodi ndi mizinda ingati imene tidaononga imene idali yochita zoipa, ndipo m’malo mwawo tidaikamo anthu ena
13.“Musathawe koma bwererani kumene mumakhala moyo wa chisangalalo ndi ku nyumba zanu kuti mukafunsidwe.”
15.Koma kulira kwawo sikunathe mpaka pamene Ife tidawaononga ndi kukhala ngati munda umene wakololedwa
18.Iyayi! Ife timatumiza choonadi kuti chilimbane ndi bodza ndipo chimaliononga. Taonani, ilo latha. Ndipo tsoka kwa inu chifukwa cha zimene mumanena
19.Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo onse amene ali pafupi pake sanyozera kumupembedza Iye ndipo satopa ayi
22.Kukadakhala milungu ina kumeneko yoonjezera pa Mulungu weniweni, ndithudi, konse kukadaonongeka. Alemekezeke Mulungu, Mwini wa Mpando wa Chifumu, mu zimene akumunenera
24.Kodi kapena iwo asankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Bweretsani umboni wanu”. Ichi ndi chikumbutso cha amene ndili nawo ndiponso iwo amakedzana. Koma ambiri a iwo sadziwa choonadi motero salabadira
25.Ndipo Ife sitidatumize iwe usadabadwe, Mtumwi wina aliyense amene sitinamuuze kuti, “Kulibe Mulungu wina koma Ine ndekha, kotero ndi pembedzeni Ine.”
26.Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabereka mwana wamwamuna.” Iye alemekezedwe! Amenewo si ena ayi koma akapolo ake olemekezeka
28.Iye amadziwa zonse zimene zili patsogolo pawo ndiponso zimene zili m’mbuyo mwawo ndipo iwo sangalankhulire wina aliyense chipulumutso kupatula amene Iye wamukonda ndipo iwo amanjenjemera chifukwa cha mantha pomuona Iye
29.Ndipo ngati wina wa iwo atanena kuti, “Ndithudi ine ndine mulungu kuonjezera pa Iye.” Oteroyo adzalangidwa ndi moto wa ku Gahena. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu olakwa
30.Kodi anthu osakhulupirira sadziwa kuti kumwamba ndi dziko lapansi chidali chinthu chimodzi chogwirana chimene tidachisiyanitsa? Ndipo tidapanga, chilichonse chamoyo, kuchokera ku madzi. Kodi iwo sangakhulupirire
31.Ndipo Ife tidakhazikitsa mapiri pa dziko lapansi molimba kuti asagwedezeke pamodzi ndi iwo ndipo tidakhazikitsa misewu pa miyala kuti mwina atsogozedwe
32.Ndipo tidapanga kumwamba denga losungika bwino limene silingagwe. Komabe iwo amakana zizindikiro zake
33.Iye ndiye amene adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi ndi china chilichonse chimene chimayenda mlengalenga
34.Palibe munthu, pambuyo pako amene tidamulenga kuti sadzafa. Ngati iweyo udzafa, kodi iwo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale
35.Chilichonse cholengedwa chidzalawa imfa ndipo Ife tidzakuyesani ndi zinthu zoipa ndi zabwino ndipo ndi kwa Ife kumene nonse mudzabwerera
36.Pamene anthu osakhulupirira amakuona iwe, sakuganizira zabwino koma chipongwe ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene amayankhula zoipa za milungu yanu?” Pamene iwo amakana zonse zokhudza Mwini chisoni chosatha
37.Munthu adalengedwa kukhala opupuluma pochita zinthu. Ine ndidzakusonyezani zizindikiro zanga. Motero musandifulumizitse
39.Akadakhala kuti anthu osakhulupirira akudziwa tsiku limene iwo sadzakhala ndi mphamvu zophimba nkhope kapena misana yawo kudziteteza ku moto ndipo iwo sangathandizike
40.Iyayi. Ilo lidzadza kwa iwo mwadzidzidzi ndipo adzadodoma ndi kusokonezeka ndipo iwo sadzatha kulibweza ndiponso sadzapatsidwa nthawi yopuma
41.Ndithudi Atumwi ena, adachitidwa chipongwe kale, koma anthu a chipongwe adafafanizidwa ndi chilango chimene iwo adachichitira chipongwe
42.Nena, “Kodi ndani adzakutetezani inu nthawi ya usiku ndi nthawi ya masana ku mkwiyo wa Mwini chisoni?” Komabe iwo salabadira zokumbukira Ambuye wawo
43.Kapena iwo ali ndi milungu ina yoti ingawateteze kwa Ife? Iyo siingathe kudziteteza yokha; ndiponso iwo sangatetezedwe kuchilango chathu
44.Koma Ife tidapereka zokoma za m’moyo uno kwa anthuwa pamodzi ndi makolo awo mpaka pamene nthawi idawatalikira iwo. Kodi iwo saona kuti Ife timachepetsa dziko lawo kuchokera m’malire mwake? Kodi iwo ndiwo adzapambane
45.Nena, “Ine ndili kukuchenjezani ndi chivumbulutso, koma agonthi sadzamva kuitana pamene achenjezedwa
46.Koma ngati katsoka kakang’ono kochokera kwa Ambuye wako kagwa pa iwo, ndithudi, iwo adzalira, “Tsoka kwa ife; ndithudi tidali anthu ochita zoipa.”
47.Ndipo Ife tidzakhazikitsa miyeso yoyenera pa tsiku la kuuka kwa akufa ndipo aliyense sadzaponderezedwa pa china chilichonse. Ngakhale patakhala ntchito zazing’ono zolingana ngati kanthangala kakang’ono tidzazitulutsa kuti ziyesedwe. Ndipo Ife ndife okwana kuwerengera ntchito zonse
49.Iwo amene amaopa Ambuye kuchokera m’maganizo a pansi penipeni pa mtima ndipo amaopa tsiku louka kwa akufa
52.Pamene Iye adawauza abambo ake ndiponso anthu ake kuti, “Kodi mafano amene muli kuwapembedzawa ndi chiyani?”
56.Iye adati, “Iyayi. Ambuye wanu ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo muzimenezo ine ndichitira umboni.”
66.Abrahamu adati, “Kodi inu mumapembedza mowonjezera pa Mulungu zinthu zimene sizingathe kukuthandizani chilichonse kapena kukuonongani?”
67.“Tsoka likhale pa inu ndi pa mafano anu amene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu! Kodi mulibe nzeru?”
71.Koma Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi Loti ndipo tidawaika ku dziko limene tidalidalitsa kuti zolengedwa zonse zikhalemo
72.Ndipo Ife tidamupatsa Isake ndi Yakobo ngati chidzukulu chake ndipo tidawapanga onse kukhala anthu angwiro
73.Ndipo Ife tidawasankha iwo kukhala atsogoleri olangiza anthu ku ulamuliro wathu ndipo tidawalamulira kuti azigwira ntchito zabwino ndipo, azipitiriza kupemphera ndi kupereka zothandizira osauka. Ndipo iwo anali kutitumikira Ife nthawi zonse
74.Ndi Loti tidamupatsa luntha, utumiki ndi nzeru za chipembedzo ndipo tidamupulumutsa ku mzinda umene anthu ake anali kuchita zoipa. Ndithudi, iwo anali anthu ochita zoipa ndipo anali osamvera Mulungu
76.Ndi pamene Nowa adatipempha poyamba, Ife tidamva pempho lake ndipo tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake ku chilango choopsa
77.Ndiponso Ife tidamupulumutsa ku gulu la anthu amene adakana chivumbulutso chathu. Ndithudi iwo anali anthu oipa ndipo onse tidawamiza m’madzi
78.Pamene Davide ndi Solomoni adaweruza mulandu wa munda umene nkhosa zosochera za anthu ena zidadya nthawiyausiku. Ndipo Ifetidalimbonipachiweruzochawo
79.Ife tidapatsa Solomoni nzeru zoweruzira nkhaniyi ndipo aliyense wa iwo tidamupatsa luntha, utumwi ndi nzeru. Tinalamula mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Davide pomutamanda Mulungu. Ndife amene tidachita zonsezi
80.Ndipo tidamuphunzitsa luso lopanga zovala za nkhondo kuti zizikutetezani pa nthawi ya nkhondo, Kodi ndinu othokoza
81.Ndi Solomoni, Ife tidampeputsira mphamvu ya mphepo. Iyo inali kuomba potsatira malamulo ake kupita kudziko limene Ife tidalidalitsa. Ndipo Ife timadziwa zinthu zonse
82.Ndipo pakati pa a Satana padali ena omwe amaimira m’malo mwa iye ndipo amachitanso ntchito zina. Kuonjezera apa ndipo ndife amene timawayang’anira iwo
83.Ndi Yobu pamene adaitana Ambuye wake nati, “Ine, ndithudi, mavuto andikuta ndipo Inu ndinu wachisoni kuposa achisoni onse.”
84.Motero Ife timamuyankha pempho lake ndipo tidamuchotsera mavuto ake ndipo tidamubwezeranso banja lake ndi zinthu zambiri zimene tidamupatsa ngati chisomo chochokera kwa Ife ndi chikumbutso kwa onse amene amatipembedza Ife
87.Ndi dhan-Nun pamene adachoka mokwiya kwambiri chifukwa iye adali kuganiza kuti Ife sitingamulenge iye. Koma mu mdima iye adaitana, “Kulibe Mulungu wina koma Inu nokha. Ulemerero ukhale kwa Inu! Ndithudi ine ndidali mmodzi mwa anthu olakwa!”
88.Motero Ife tidayankha pempho lake ndipo tidamupulumutsa ku mavuto ake. Motero ndimo mmene timapulumutsira anthu okhulupirira
89.Ndi Zakariya pamene anaitana Ambuye wake nati, “Ambuye wanga! Musandileke ndekha. Ndipo Inu ndinu wabwinomwaokhalitsaonse.”
90.Motero Ifetidamuyankha pempho lake ndipo tidamupatsa Yohane ndipo tidathetsa uchumba wa mkazi wake. Ndithudi iwo adali ofulumira pochita ntchito zabwino ndipo amatipempha Ife ndi chikhulupiriro ndi mantha ndiponso amadzichepetsa kwa Ife
91.Adali mkazi amene adasunga unamwali wake. Ife tidauzira mwa iye ndipo tidamupanga iye pamodzi ndi mwana wake wa mwamuna kukhala chizindikiro kwa zolengedwa zonse
92.Ndithudi! Ichi ndi chipembedzo chanu ndipo ndi chipembedzo chimodzi, ndipo Ine ndine Ambuye wanu motero ndipembedzeni Ine ndekha
93.Ndipo iwo adapatukana ndi kugawa chipembedzo chawo pakati pawo ndipo ndi kwa Ife kumene adzabwerera
94.Motero aliyense amene achita ntchito zabwino ndipo ndi wokhulupirira moona ntchito zake sizidzakanidwa ayi. Ndithudi Ife timazilemba zonse m’Buku la chiwerengero
96.Mpaka pamene anthu a Ya-juj ndi Majuj adzamasulidwa ndipo iwo adzakhala akutsika kuchokera kumalo aliwonse wokwera
97.Ndipo pamene lonjezo loona lidzafika, maso a anthu onse osakhulupirira adzapenyetsetsa mwamantha nati “Tsoka kwa ife! Ndithudi ife tidali osalabadira zimenezi. Zoonadi ife tidali ochita zoipa.”
98.Ndithudi! Inu pamodzi ndi zimene mukupembedza kuonjezera pa Mulungu, mudzakhala nkhuni za ku Gahena! Kumeneko nonse mudzalowako
103.Zoopsa sizidzawadandaulitsa ayi ndipo Angelo adzawalandira iwo nati,“Ili ndi tsiku lanu limene inu mudalonjezedwa.”
104.Tsiku limene tidzapinde thambo monga momwe timapindira tsamba la Buku. Monga momwe tidayamba chilengedwe choyamba momwemonso tidzachibwezeranso. Ili, ndithudi, ndi lonjezo kwa Ife. Ndithudi, Ife, tidzachita motero
105.Ndipo, ndithudi, Ife tidalemba m’Buku la Masalimo, motsatira chikumbutso kuti akapolo anga angwiro adzakhala ku dziko lapansi
108.Nena, “Zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi yekha. Kodi inu mudzadzipereka kwa Iye?”
109.Koma ngati iwo safuna kumvera nena, “Ine ndili kukuchenjezani kuti tonse tidziwe. Ine sindidziwa kuti chimene mwalonjezedwa chidza msanga kapena chikadali patali.”
112.Iye anati, “Ambuye wanga! Weruzani mwachilungamo! Ambuye wathu ndi Mwini chisoni chosatha amene chithandizo chake chimafunika pa zimene inu muonjezera.”