الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Alif Lam Mim
61.Ndi pamene mudati: “oh Mose! Ife sitingapirire kudya chakudya chamtundu umodzi. Motero tipemphere kwa Ambuye wako kuti atitulutsire zina mwa zomera m’nthaka monga masamba, minkhaka, tirigu, nyemba ndi anyezi.” Iye adati: “Kodi inu mufuna kusinthitsa chinthu chabwino ndi choipa? Pitani ku mzinda uliwonse ndipo kumeneko mudzapeza zonse zimene mufuna.” Ndipo manyazi ndi umphawi udadza pa iwo ndipo iwo adapalamula mkwiyo wa Mulungu chifukwa iwo adali kukana mau a Mulungu ndipo anali kupha Atumwi popanda chifukwa popeza iwo adali anthu aupandu ndi anthu osamvera
85.Zitatha izi ndinu amene mudayamba kupha abale anu ndi kupirikitsa gulu lina la inu m’nyumba zawo ndi kuthandiza adani awo pochita machimo ndi kuswa malamulo. Ndipo iwo akamabwera kwa inu ngati akapolo, inu muwaombola ngakhale kuti kupilikitsidwa kwawo kudali koletsedwa kwa inu. Kodi inu mukhulupirira gawo lina la Mau a Mulungu ndi kukana gawo linzake? Kodi ndi malipiro otani amene angalandire wochita zimenezo mwa inu, kupatula mphotho yochititsa manyazi m’dziko lino ndi chilango chowawa kwambiri patsiku louka kwa akufa? Mulungu saiwala ntchito zanu zimene muchita
102.Iwo adatsatira zimene a Satana adanena mu Ufumu wa Solomoni. Sikuti Solomoni sadakhulupirire ai koma a Satana ndiwo sadakhulupirire. Iwo amaphunzitsa anthu matsenga ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa angelo awiri Harut ndi Marut ku Babuloni. Koma iwo samaphunzitsa wina aliyense mpaka atanena kuti: “Ndithudi ife tili kukuyesani inu, ndipo musakhale wosakhulupirira ayi.” Kuchokera kwa angelo chimene chimamasula pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndipo iwo sadaononge wina aliyense ndi zimene adaphunzira kupatula ndi chilolezo cha Mulungu. Iwo amaphunzira zinthu zimene zimawaononga ndipo sizidawapindulire china chilichonse. Ndithudi iwo amadziwa kuti aliyense amene amachita matsenga sadzakhala ndi gawo m’moyo umene uli nkudza. Zopanda pake ndi zimene agulitsa nazo moyo wawo, iwo akadadziwa
177.Chilungamo sichili m’machitidwe oti muziyang’ana ku m’mawa kapena ku madzulo, koma chilungamo ndi kukhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, mwa angelo ndi Buku la Mulungu, mwa Atumwi ndiponso kupereka chuma chimene amachikonda kwa abale ake, kwa a masiye, kwa anthu osauka, kwa a paulendo, kwa anthu opempha ndi kuombola a kapolo. Ndipo onse amene amasamala mapemphero ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndi amene amakwaniritsa lonjezo lawo akalonjeza ndipo amakhala opirira pa mayesero ndi m’mavuto ndiponso m’nthawi za nkhondo, amenewa ndiwo okhulupirira enieni ndiponso amenewa ndiwo amene amaopa Mulungu
185.M’mwezi wa Ramazani ndi mmene Korani idavumbulutsidwa. Iyo ndi ulangizi kwa anthu ndi umboni wooneka wolangiza ndi kusiyanitsa. Motero aliyense wa inu amene wauona mwezi umenewu, ayenera kusala. Koma yense amene ali kudwala kapena ali paulendo, adzasale masiku ofanana ndi amene sadasale. Mulungu akufuna kukupeputsirani zinthu osati kuonjeza masautso ayi. (Iye) afuna kuti mukwaniritse kusala masiku onse olamulidwa ndiponso muyenera kumalemekeza Mulungu chifukwa chokutsogolerani kuti mukhale othokoza
187.Ndikololedwa kwa inu kugona ndi akazi anu mu usiku wa kusala. Iwo ndi chofunda chanu pamene nanu ndi chofunda chawo. Mulungu amadziwa kuti munali kudzinyenga nokha pogona nawo opanda chilolezo. Iye adavomera kulapa kwanu ndipo adakukhululukirani. Tsopano mukhoza kugona nawo ndipo funani zimene Mulungu wakulamulirani inu. Idyani ndi kumwa mpaka pamene mukhoza kusiyanitsa pakati pa ulusi woyera ndi wakuda pamene kuli nkucha. Ndipo pitirizani kusala mpaka pamene dzuwa lilowa ndipo musawakhudze akazi anu pamene muli kubindikira m’mapemphero. Amenewa ndi malire a Mulungu ndipo musawayandikire ayi. Motero Mulungu amafotokoza chivumbulutso chake kwa anthu kuti akhale omuopa Iye
196.Kwaniritsani miyambo ya Hajji ndi Umra chifukwa cha Mulungu. Ndipo ngati mwatsekerezedwa, iphani, ngati nsembe, nyama zimene sizili zovuta kuzipeza ndipo musamete mitu yanu mpaka nyama zitafika pa malo ake ophera. Koma aliyense wa inu amene ndi wodwala kapena ali ndi vuto m’mutu mwake ayenera kudziombola posala kapena kupereka nsembe kapena kupha nyama. Ngati muli pa mtendere ndiponso wina wa inu aphatikiza Umra ndi Hajji, ayenera kupha nyama imene angaipeze mosavutikira kwambiri. Koma ngati sangathe kuipeza ayenera kusala masiku atatu pa nthawi ya Hajji ndi masiku asanu ndi awiri akabwerera kwawo; amenewo ndi masiku khumi okwana. Zimenezi ndi za iye amene banja lake silili pafupi ndi Mzikiti Woyera. Muopeni Mulungu. Ndipo dziwani kuti Mulungu amakhwimitsa chilango
213.Anthu onse anali mtundu umodzi ndipo Mulungu adatumiza Atumwi kudzawauza nkhani yabwino ndi kuwachenjeza ndipo ndi iwo adatumiza mau ake mwa choonadi kuti aweruze pa mikangano imene ili pakati pawo. Ndipo okhawo amene adaperekedwa amatsutsa za ilo iwo atalandira zizindikiro zooneka chifukwa cha udani wa wina ndi mzake. Ndipo Mulungu analangiza mwa chifuniro chake iwo amene amakhulupirira m’choonadi chimene chinali kutsutsidwa. Ndipo Mulungu amatsogolera wina aliyense amene wamufuna ku njira yoyenera
217.Iwo akukufunsa zomenya nkhondo M’mwezi Woyera. Nena: “Kumenya nkhondo m’mwezi uwu ndi kulakwa kwakukulu koma kulakwa kwakukulu zedi pamaso pa Mulungu ndi kutsekereza anthu kuti atsatire njira ya Mulungu, kumukana Iye ndi kuletsa anthu kulowa mu Mzikiti Woyera ndi kupirikitsa anthu ake opembedza m’menemo. Ndipo kuchita zinthu zosokoneza chipembedzo ndi koipa kwambiri kuposa kupha munthu.” Ndipo iwo sadzasiya kumenyana nanu mpaka atakuchotsani mchipembedzo chanu ngati angathe kutero. Ndipo aliyense wa inu amene adzasiye chipembedzo chake chenicheni ndipo afa ali osakhulupirira, ntchito zake zonse zidzakhala zopanda pake m’dziko lino ndiponso m’dziko limene lili nkudza. Anthu otere adzakhala eni ake a ku Gahena ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale
221.Musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndipo, ndithudi, kapolo wachikazi wokhulupirira ali bwino kuposa mfulu yaikazi yopembedza mafano ngakhale atakukondweretsani. Ndiponso musadzakwatitse aliyense wopembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi kapolo wokhulupirira ali bwino kuposa mfulu yopembedza mafano ngakhale kuti iye wakusangalatsani. Iwo amakuitanirani ku moto pamene Mulungu amakuitanirani ku Paradiso ndi ku chikhululukiro mwachifuniro chake, ndipo Iye amafotokoza bwino bwino chivumbulutso chake kwa anthu kuti mwina akhoza kukumbukira
229.Chisudzulo ndi chololedwa kawiri kokha ndipo pambuyopake,mukhozakukhalanayelimodzimogwirizana kapena kusiyana mwaulemu. Ndi choletsedwa kwa inu amuna kutenga katundu wina aliyense amene mudawapatsa akazi anu pokhapokha ngati onse awiri aopa kuti sadzatha kukwaniritsa malamulo a Mulungu. Ndipo ngati inu muopa kuti iwo sadzakwaniritsa malamulo a Mulungu, palibe mlandu kwa iwo ngati mkazi apereka mphatso kapena gawo lake ngati chodziombolera. Awa ndi malamulo a Mulungu ndipo musawaswe. Ndipo aliyense amene aswa malamulo amene anakhazikitsa Mulungu, wotere ndiwo olakwa
233.Amayi adzayamwitsa ana awo zaka ziwiri zathunthu, izi ndi za makolo amene afuna kukwaniritsa kuyamwitsa. Koma ndi udindo wa atate kupereka chakudya ndi zovala za amai potsatira malamulo. Munthu sadzanyamula chinthu chimene sangathe kuchichita. Mayi asazunzidwe chifukwa cha mwana wake kapena bambo asavutitsidwe chifukwa cha mwana wake. Udindo umenewu umagweranso aliyense amene alowa chokolo. Koma ngati onse agwirizana kuti amuletse kuyamwa mwana, iwo sadzakhala ndi mlandu. Ngati inu muganiza kuti wina akuyamwitsireni mwana wanu, sikulakwa ngati inu mumulipira mtengo umene mwagwirizana. Ndipo opani Mulungu, ndipo dziwani kuti Mulungu amaona zimene muchita
246.Kodi iwe siudawone zimene gulu la ana a Israyeli adachita Mose atafa? Pamene iwo adati kwa Mtumwi wawo: “Tisankhire Mfumu,” ndipo ife tidzamenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Iye adati: “Kodi inu simungamenye nkhondo ngati mutalamulidwa kutero?” Iwo adati: “Kodi ife tingakane bwanji kumenya nkhondo mmene afunira Mulungu pamene ife tidaumilizidwa kuchoka m’nyumba mwathu ndi kusiya ana athu?” Koma pamene adalamulidwa kuti amenye nkhondo, onse adathawa kupatula anthu owerengeka okha. Ndipo Mulungu amadziwa anthu osalungama
249.Ndipo pamene Saulo ananyamuka ndi gulu lake la nkhondo, iye adati: “Ndithudi! Mulungu adzakuyesani pa mtsinje. Motero aliyense amene adzamwa madzi pamenepo sadzakhala wa gulu langa, ndipo yense amene sadzamwa adzakhala wa gulu langa, kupatula yekhayo amene adzatunge muyeso wa pa chikhato pake.” Koma padali kagulu kochepa kamene kadamwa motero. Motero iye atawoloka mtsinjewo, iye ndi iwo amene adakukhulupirira mwa iye, adati: “Ife lero tilibe mphamvu zogonjetsera Goliati ndi Asirikali ake.” Koma iwo amene adali ndi chikukhulupiriro choti adzakumana ndi Ambuye wawo adati: “Kodi ndi kangati kagulu kochepa kamagonjetsa chigulu cha nkhondo ndi chilolezo cha Mulungu? Ndipo Mulunguamakhalapamodzindiopirira.”
253.Atumwi aja! Ife tidawakweza ena kuposa anzawo. Kwa ena a iwo Mulungu adalankhula nawo mwachindunji, pamene ena adawakweza kukhala a pamwamba ndipo kwa Yesu mwana wa Mwamuna wa Maria, Ife tidampatsa zizindikiro zooneka ndipo tidamulimbikitsa ndi Mzimu Woyera. Mulungu akadafuna, iwo amene adadza pambuyo pawo sakadamenyana wina ndi mnzake pamene zizindikiro zooneka zitadza kwa iwo, koma iwo adakangana. Ena adali ndi chikhulupiriro pamene ena mwa iwo adakana. Koma Mulungu akadafuna, iwo sakadamenyana wina ndi mzake ayi. Mulungu amachita chimene wafuna
255.Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha, wamoyo ndi wamuyaya. Iye saodzera kapena kugona. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Ndani amene angakhale mkhalapakati pa Iye opanda chilolezo chake? Iye amadziwa zonse zimene zimachitika mdziko lino ndi zimene zidzachitike m’moyo uli nkudza. Ndipo iwo sadzadziwa chilichonse kuchokera ku nzeru zake pokhapokha ngati Iye afuna. Mpando wake umafika kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo chisamaliro chake pazinthu zonse sichimutopetsa ayi. Iye ndi wapamwamba mwamba ndi Wamkulu zedi
259.Kapena iye amene adadutsa Mumzinda umene udaonongeka ndi kusanduka bwinja ndipo adanena kuti: “Kodi Mulungu angapereke moyo bwanji ku Mzinda pamene utafa?” Motero Mulungu adamupha iye ndipo patatha zaka zana limodzi Iye adamuukitsa kwa akufa. Mulungu adati: “Kodi iwe wakhala chifere nthawi yotani?” Iye adati: “Mwina tsiku limodzi kapena maola owerengeka basi.” Mulungu adati: “Iyayi, iwe wakhala zaka zana limodzi. Taona chakudya chako ndi chakumwa chako, sizinasinthe ayi ndipo taona bulu wako! Ife tikusandutsa kuti ukhale chizindikiro kwa anthu. Ndipo taona mafupa m’mene timawaikira pamodzi ndi kuwakuta ndi mnofu.” Ndipo pamene zonse zinaonetsedwa kwa iye, iye adati: “Ndadziwa tsopano kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”
275.Iwo amene amadya ndalama za katapira, adzaima maimidwe a munthu amene wamenyedwa ndi Satana ndi kumuyambitsa misala. Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amanena kuti: “Katapira ali chimodzimodzi ndi kugulitsa malonda.” Pamene Mulungu adaloleza malonda, Iye adakaniza katapira. Ndipo iye amene alandira chidzudzulo kuchokera kwa Ambuye wake, ndipo aleka, adzakhululukidwa zochimwa zake zakale koma nkhani yake ili m’manja mwa Mulungu. Koma iye amene abwerezanso kudya ndalama za katapira iye adzaponyedwa ku moto wa ku Gahena ndipo iwo adzakhala komweko mpaka kalekale
282.oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukongola ngongole yoperekedwa panthawi yomwe mwagwirizana, lembani pena pake. Mlembi alembe zonse mwachilungamo. Ndipo iye asakane kulemba monga mmene Mulungu wamuphunzitsira, motero alembe. Ndipo mulekeni wokongolakutianenezotizilembedwendipoayenerakuopa Mulungu Ambuye wake ndipo iye asabise mangawa ena aliwonse amene ali nawo. Koma ngati munthu wokongolayo ndi wozerezeka kapena wofoka kapena amene sangathe kuyankhula, muloleni m’bale wake kuti ayankhule m’malo mwa iye komatu mwachilungamo. Ndipo itanani amuna awiri amene ali pakati panu kuti akhale mboni. Ndipo ngati anthu amuna sangathe kupezeka, funani mwamuna mmodzi ndi akazi awiri amene mungavomereze kukhala mboni, kuti achitire umboni; kuti ngati wina wa iwo alakwa, wina adzakumbutse mnzake. Ndipo mboni zisamakane kupereka umboni ngati ziitanidwa kutero. Kotero musatope kulemba ngongole zanu kaya ndi yaing’ono kapena yaikulu, ndipo mulembenso tsiku lodzabwezedwa ngongoleyi. Ichi ndicho chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo zimakhala dongosolo pofuna kutsimikiza ndiponso ndi njira yabwino kuti musakaike kupatula ngati zimene zili kugulitsidwa ndi zinthu zopezeka mwa mwayi ndipo ndi zoti zigulitsidwe msangamsanga, si mlandu ngati inu simulemba. Koma onetsetsani kuti pali mboni pamene muli kugulitsana wina ndi mnzake. Ndipo pasakhale vuto kwa mlembi kapena wochitira umboni koma ngati mutero mudzalakwa. Motero opani Mulungu chifukwa amakuphunzitsani inu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
286.Mulungu sapereka katundu wolemera pa mzimu umene siungathe kumunyamula. Mzimuuliwonseumalandirachilichonsechabwinochimene umachita kapena umalangidwa chifukwa cha ntchito zake zoipa zimene umachita. Pemphani kuti: “Ambuye wathu! Musatilange ife ngati tiiwala kapena tilakwa. Ambuye wathu! Musatikundikire ife mavuto monga amene mudakundikira anthu amene adalipo kale. Ambuye wathu! Musatisenzetse zinthu zimene sitingathe kuzinyamula. Tichotsereni machimo, tikhululukireni ndipo tichitireni chifundo ife. Inu nokha ndinu Mtetezi wathu. Tipatseni kupambana pakati pa anthu osakhulupirira.”