4.Iye adati, “oh Ambuye wanga! Mafupa anga ndi ofoka ndipo mutu wanga uli ndi imvi chifukwa cha ukalamba. Komabe, Ambuye, ine sindidapemphe kwa Inu mopanda phindu.”
5.“Ndithudi ine ndili ndi mantha ndi abale anga za amene adzalowe m’malo mwanga ndiponso mkazi wanga ndi chumba. Ndipatseni mwana wamwamuna.”
6.“Amene adzalowe m’malo mwanga ndi m’malo mwa ana a Yakobo, ndipo mpangeni, Ambuye wanga, kukhala mmodzi wa wokondedwa wanu.”
7.“Ee iwe Zakariya! Ife tili kukuuza nkhani yabwino yakuti iwe udzapatsidwa mwana wamwamuna ndipo adzatchedwa Yohane, dzina limene silidapatsidwe kwa aliyense kumbuyoku.”
8.Zakariya adati, “Ambuye! Kodi ine ndingakhale ndi mwana wamwamuna bwanji, pamene mkazi wanga ndi chumba ndipo ine ndine wokalamba?”
9.Iye adati, “Chimenechi, wanena Ambuye wako! Idzakhala ntchito yopepuka kwa Ine chifukwa Ine ndidakupanga kukhala munthu pamene iwe siunali chinthu china chilichonse chodziwika.”
10.Zakariya adati, “Ambuye, ndipatseni chizindikiro chokhudza zimene zidzachitike.” Iye adati, “Chizindikiro chako ndi chakuti siudzalankhula ndi anthu usiku utatu ngakhale ulibe chilema.”
11.Pamene Zakariya adadza kwa anthu ake kuchokera m’kachisi, adawauza anthuwo kuti, “Lemekezani Ambuye wanu m’mawa ndi madzulo.”
14.Ndipo adali kulemekeza abambo ndi amayi ake. Iye sadali wodzikweza kapena wonyoza malamulo a Mulungu
15.Mtendere udali pa iye pa tsiku limene adabadwa ndi pa tsiku limene adafa ndipo mtendere ukhale pa iye pamene aukitsidwa kwa akufa
16.Ndipo kukumbukira nkhani ya Maria m’Buku! Pamene iye adasiya anthu ake ndi kupita kumalo a payekha kumbali ya ku m’mawa
17.Ndipo iye adafunda nsalu kuti anthu asaone nkhope yake. Ife tidamutumizira iye Mzimu wathu umene udaoneka ngati munthu
18.Maria adati, “Mwini chisoni anditeteze ine kwa iwe! Ngati iwe umaopa Ambuye, ndisiye ndekha, usandiyandikire ayi.”
19.Mngelo adati, “Ine ndine Mthenga wa Ambuye wako ndipo ndadza kudzakupatsa mwana wamwamuna woyera.”
20.Maria adati, “Kodi ine ndidzabereka mwana bwanji pamene ine ndine wosakhudzidwa ndi mwamuna ndiponso si ndine wachiwerewere ayi?”
21.Mngelo adati, “Ndi momwemo” Ambuye wako wanena kuti, “Zimenezo, kwa Ine, ndi zopepuka. Tidzamupanga iye kukhala chizindikiro kwa anthu ndi madalitso ochoka kwa Ife. Limeneli ndilo lamulo limene lalamulidwa.”
23.Ndipo ululu wa kubereka udamubwerera pamene adali patsinde pa mtengo wa tende ndipo adalira nati, “Kalanga ine, bola ndikadangofa zisanachitike izi chifukwa ndikadakhala woiwalidwa.”
24.Kudabwera mawu kuchokera pansi oti: “Usadandaule ayi. Ambuye wako wakukonzera ka mtsinje kamene kalikuyenda ku mapazi ako.”
26.“Idya ndi umwe, kotero sangalala.” Ndipo ukakumana ndi munthu wina aliyense muuze kuti, “Ine ndalumbira kwa Mwini chisoni kusala chakudya ndipo sindidzayankhula ndi munthu wina aliyense lero.”
27.Ndipo iye adatenga mwana wake nanka naye kwa anthu ake amene adati kwa iye’ “Iwe Maria! Ndithudi iwe wabweretsa chinthu cha chilendo.”
28.“Iwe mlongo wake wa Aroni! Atate wako sanali munthu wochita zoipa ndiponso Amayi ako sadali a chiwerewere.”
30.Mwanayo adati, “Ine ndine kapolo wa Mulungu. Iye wandipatsa ine Buku labwino ndipo wandisankha kukhala Mtumwi.”
31.“Madalitso ake ali pa ine kulikonse kumene ndingapite ndipo wandilamulira kuti ndikhale wopemphera ndi kupereka chaulere kwa anthu osauka nthawi yonse ya moyo wanga.”
33.Ndipo mtendere ukhale kwa ine patsiku limene ndidabadwa, ndi patsiku limene ndidzafa ndiponso pa tsiku limene ndidzaukitsidwa kwa akufa
35.Sizili zoyenera kuti Mulungu akhale ndi mwana wamwamuna! Iye ayeretsedwe ku zimenezo. Ngati Iye afuna chinthu, Iye amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi
36.Ndithudi Mulungu ndi Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Kotero mpembedzeni Iye yekha. Imeneyo ndiyo njira
37.Koma magulu a Akhirisitu adasemphana maganizo pakati pawo. Koma pamene tsiku loopsa lidza, tsoka kwa anthu osakhulupirira
38.Kodi iwo adzaona ndi kumva momveka bwanji pa tsiku limene adzaonekera pa maso pathu! Koma anthu ochita zoipa lero ali mu chisokonezo choonekeratu
39.Achenjeze za tsiku limene adzanong’oneza bombono, pamene malamulo athu adzakwaniritsidwa ndipo pamene iwo ali nkuiwala ndi kusakhulupirira
40.Ndithudi Ife tidzatenga dziko lapansi ndi onse amene amakhala m’menemo. Ndi kwa Ife kumene onse adzabwezedwa
42.Pamene iye adawauza bambo wake kuti, “Oh Abambo! Kodi inu mungalambire bwanji chinthu chimene sichingathe kumva, kuona kapena kukuthandizani pa chilichonse?”
43.“Ohabambo! Choonadichavumbulutsidwa kwa ine chimene sichinakufikireni inu. Kotero nditsatireni ine kuti ndikutsogolereni ku njira yoyenera.”
45.“oh abambo! Ine ndili kuopa kuti chilango cha Mulungu chidzadza pa inu ndipo mudzakhala bwenzi la Satana.”
46.Abambo ake adati, “Kodi ukudana ndi milungu yanga iwe Abrahamu? Ukapanda kusiya ndidzakuponya miyala ndipo unditalikire pa kanthawi kochepa.”
47.Abrahamu adati, “Mtendere ukhale kwa inu. Ine ndidzapempha Ambuye wanga kuti akukhululukireni popeza, Mulungu, kwa ine, ndi wokoma mtima.”
48.“Ine ndikuchokerani ndi zimene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu. Ine ndidzapempha kwa Ambuye wanga ndipo ndikhulupirira kuti popembedza Ambuye wanga ndisadzakhale watsoka
49.Ndipo pamene Abrahamu adasiya anthu ake ndi mafano amene iwo anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu, tidamupatsa Isake ndi Yakobo. Aliyense wa iwo tidamupanga kukhala Mtumwi
50.Ndipo tidawapatsa onse mituka kuchokera m’chifundo chathu ndipo tidawapanga iwo kukhala otchulidwa mwaulemu
51.Ndipo kumbukira nkhani ya Mose imene ili m’Buku, amene adali wosankhidwa ndiponso Mtumwi ndi Mneneri
52.Ife tidamuitana kuchokera kumbali ya dzanja la manja la phiri la Sinai ndipo tinamuyandikitsa kukhala pafupi ndi Ife kuti tiyankhule naye mwamseri
54.Ndipo kumbukira nkhani ya Ishimayeli imene ili m’Buku. Iye adali wosunga pangano ndipo adali Mtumwi ndi Mneneri
55.Iye anali kulamula anthu ake kuchita mapemphero ndi kupereka chothandiza nacho anthu osauka ndipo adali, kwa Ambuye wake, wokondedwa
58.Awa ndi anthu amene Mulungu adawaonetsera chisomo chake. Atumwi ochokera ku m’badwo wa Adamu ndi iwo amene tidawatenga pamodzi m’chombo ndi Nowa. Ana a Abrahamu, a Israyeli ndi iwo amene Ife tawatsogolera ndi kuwasankha. Pamene zivumbulutso za Mwini chisoni chosatha zinali kulakatulidwa kwa iwo, iwo adali kugwa nkhope zawo pansi ndi kumalira
59.Koma mibadwo ya anthu imene inadza iwo atachoka idanyoza mapemphero ndi kutsatira zilakolako zawo. Ndithudi awa adzakumana ndi mavuto
60.Kupatula amene alapa machimo ndi kukhulupirira choonadi ndi kumachita ntchito zabwino. Iwo adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa m’chilichonse
61.Iwo adzakhala m’minda ya Edeni mpaka muyaya, imene Mwini chisoni chosatha adalonjeza akapolo ake ngakhale kuti iwo sadaione. Ndithudi lonjezo lake lidzakwaniritsidwa
62.Kumeneko iwo sadzamva zinthu zopanda pake koma mawu a mtendere okha, ndipo chakudya chidzapatsidwa kwa iwo m’mawa ndi madzulo
64.Ife sititsika kuchoka kumwamba pokhapokha ngati taloledwa ndi Ambuye wako. Iye ndiye mwini wa zinthu zonse zimene zili pamaso pathu, kumbuyo kwathu ndi zonse zimene zili pakati pa zimenezi. Ndipo Ambuye wako saiwala
65.Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo. Kotero m’pembedze Iye yekha ndipo khala wopirira pamapemphero ake. Kodi ukudziwa wina amene ali ndi dzina ngati la Iye
68.Motero pali Ambuye wako; ndithudi Tidzawasonkhanitsa pamodzi ndi a Satana ndipo onse tidzawabweretsa m’mphepete mwa Gahena atagwada
71.Palibe wina wa inu amene sadzapita kumbali ya Moto. Limeneli ndilo lamulo la mphamvu la Ambuye wanu
72.Ndipo Ife tidzapulumutsa onse amene amaopa ndi kuwasiya ochita zoipa, atagwada, kuti amve ululu wake
73.Pamene zivumbulutso zathu zilakatulidwa momveka kwa iwo, anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ndi gulu liti pa magulu awiriwa limene lili ndi malo abwino okhala ndi anthu apamwamba?”
74.Kodi ndi mibadwo ingati yakale imene tidaononga iwo asanadze, mibadwo imene idali ndi zinthu zabwino ndiponso zokongola
75.Nena, “Aliyense amene alakwa, Mwini chisoni chosatha adzawaonjezera nthawi, mpaka pamene adzaone zomwe adalonjezedwa. Kaya ndi chilango kapena ola lomaliza, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndani amene ali mwini wa malo oipa ndi gulu lankhondo lofoka.”
76.Mulungu amapitiriza kutsogolera iwo amene atsatira njira yoyenera. Ntchito zabwino zimene zili ndi malipiro osatha zili ndi mphotho yabwino pamaso pa Ambuye wako ndiponso zotsatira zake ndi zabwino
77.Kodi mwamuona munthu amene akana zivumbulutso zathu ndipo amanena kuti, “Ine, ndithudi, ndidzapatsidwa chuma ndi ana?”
83.Kodi siudaone kuti timatumiza kwa anthu osakhulupirira a Satana amene amawaonetsa zinthu zoti achimwe nazo
85.Tsiku limenetidzasonkhanitsaanthuolungamam’magulu kufika pamaso pa Ambuye wachisoni kudzalandira ulemu
87.Palibe amene adzakhala ndi mphamvu zodandaula kupatula yekhayo amene walandira chilolezo cha Mwini chisoni chosatha
90.Pafupifupi kumwamba kumafuna kung’ambika chifukwa cha mawu amenewa ndipo nthaka imafuna kugawikana ndi mapiri kugudubuzika ndi kuonongeka
93.Palibe china chilichonse chimene chili kumwamba kapena pa dziko lapansi chimene chimabwera kwa Mwini chisoni chosatha kupatula ngati kapolo
97.Motero Ife tapanga iyo kukhala yosavuta ya m’chiyankhulo chako kuti upeleke nkhani yabwino kwa anthu oopa ndi kuchenjeza ndi ilo anthu otsutsa
98.Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga kale iwo asanadze? Kodi uli kumuona mmodzi aliyense wa iwo kapena kumva manong’onong’o ochokera kwa iwo