الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Alif Lam Mim Raa. Awa ndi mavesi a Buku. Chimene chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako ndi choonadi. Koma anthu ambiri sakhulupirira
16.Nena, “Kodi Ambuye wakumwamba ndi pa dziko lapansi ndani?” Nena, “Mulungu.” Nena, “Kodi inu mwasankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni imene, ngakhale kwa iyo yokha, singathe kuchita zinthu zoipa kapena zabwino?” Nena, “Kodi anthu a khungu ndi anthu oona ndi ofanana? Kapena mdima umafanana ndi kuwala? Kodi iwo akuphatikiza Mulungu ndi mafano awo? Kodi mafano awo adalenga zinthu zofanana ndi zimene Iye adalenga; kotero kuti zolengedwa zonse zimaoneka kwa iwo ngati zofanana?” Nena, “Mulungu ndi Namalenga wa zinthu zonse. Iye ndi Mmodzi yekha ndipo ndi Mwini Mphamvu zonse.”