الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Alif Lam Ra. Awa ndi mawu a Buku lofotokoza bwino
100.Ndipo iye adanyamula makolo ake ndikuwakhazika pa mpando wolemekezeka ndipo onse adagwa pansi kulemekeza iye. Ndipo iye adati, “Oh bambo wanga! Ili ndi tanthauzo la maloto anga aja akale. Ndithudi Ambuye wanga adawapanga kukhala oona. Iye adandichitira ine ubwino pamene adanditulutsa kundende ndipo adakubweretsani inu kuchokera ku midzi pambuyo pakuti satana adakhazikitsa udani pakati pa ine ndi abale anga. Ndithudi Ambuye wanga ndi waulemu ndi wachisoni kwa amene Iye wamufuna. Ndithudi! Iye yekha ndi wodziwa zonse ndi wanzeru.”