٤.Ndi pali Bait – Ul-Ma’mur (Nyumba imene ili kumwamba yolingana ndi Kaaba imene ili ku Makka ndipo imaonedwa ndi angelo pafupipafupi)
١٦.Lawani kutentha kwake ndipo kaya inu mupirira kapena ayi, kwa inu ndi chimodzimodzi; inu muli kulandira malipiro a ntchito zomwe mumachita
١٨.Kusangalala chifukwa cha zimene Ambuye wawo wawapatsa ndipo Ambuye wawo wawapulumutsa ku chilango cha ku Gahena
٢٠.Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo, yoikidwa m’mizere. Ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa amene ali ndi maso akuluakulu ndi okongola
٢١.Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo ana awo amawatsatira m’chipembedzo, oterewa tidzawakumaniza ndi mabanja awo ndipo Ife sitidzawachotsera chilichonse cha malipiro a ntchito zawo zabwino. Munthu aliyense adzafunsidwa malinga ndi ntchito zake
٢٤.Iwo adzazunguliridwa ndi kutchingidwa bwino ndi anyamata awoawo amene adzawatumizira ngati kuti iwo anali ndolo zobisika
٢٨.“Ndithudi ife tinali kumupempha Iye yekha. Ndithudi Iye ndiye Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.”
٢٩.Motero pitiriza kukumbutsa ndi kulalikira. Chifukwa cha chisomo cha Ambuye wako, iwe si ndiwe munthu wonyenga kapena wamisala
٣٢.Kodi ndi maganizo awo amene ali kumawauza izi kapena iwo ndi anthu amene amaswa malamulo mosadodoma
٣٦.Kapena ndiwo amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro chokhazikika
٣٧.Kodi ndiwo amene amasunga chuma cha Ambuye wako? Kapena iwo ndiwo a nkhanza amene ali ndi ulamuliro wonena chilichonse chimene afuna
٣٨.Kodi kapena iwo ali ndi njira yomvetsera zomwe zinali kunenedwa? Motero mulekeni kazitape wawo kuti apereke umboni wokwanira
٤٣.Kodi kapena ali ndi mulungu wina kupatula Mulungu weniweni? Mulungu alemekezeke kuposa zimene iwo amamufanizira nazo
٤٤.Ndipo iwo akadaona gawo lina la kumwamba lili kugwa pansi ndipo iwo akadati, “Ndi mitambo youndana.”
٤٦.Tsiku limene chiwembu sichidzawathandiza china chilichonse ndipo chithandizo sichidzaperekedwa kwa iwo
٤٧.Ndipo, ndithudi, onse amene amachita zoipa, kuli chilango china pa chilango ichi koma ambiri a iwo sadziwa
٤٨.Motero pirira podikira chiweruzo cha Ambuye wako, chifukwa ndithudi iwe uli kusamalidwa ndi Ife ndipo lemekeza Ambuye wako pamene uuka ku tulo