٤.M’chilengedwe chanu nyama zimapezeka paliponse pa dziko lapansi ndipo ndi zizindikiro kwa iwo amene ali okhulupirira kwenikweni
٥.Ndi m’kasinthidwe ka usiku ndi usana ndi m’chakudya chimene amatumiza kuchokera ku mitambo ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali yakufa ndipo m’kasinthidwe ka mphepo, muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
٦.Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Mulungu chimene tili kulakatula kwa iwe mwachoonadi. Nanga ndi uthenga uti wa Mulungu ndi chivumbulutso chake chiti chomwe iwo akhoza kukhulupirira
٨.Amene amamva mawu a Mulungu amene ali kunenedwa kwa iye ndipo amapitirizabe kunyada ngati iye sanamve. Motero muuze iye za chilango chowawa
٩.Ndipo pamene iye akamva mawu a Mulungu, amawasandutsa kukhala masewera. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chochititsa manyazi
١٠.Kutsogolo kwawo kuli Gahena, ndipo sadzapeza phindu lina lililonse pa ntchito zawo kapenakwaiwoameneadawasandutsakukhalawowasamala poonjezera pa Mulungu. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa
١١.Ichi ndi chilangizo choona. Ndipo iwo amene amakana zizindikiro za Ambuye wawo, adzalandira chilango chapadera chowawa
١٢.Ndi Mulungu amene adachepetsa mphamvu ya nyanja kuti masitima aziyenda mwaulamuliro wake ndipo kuti inu mukhoza kufuna chisomo chake kuti muzimuthokoza
١٣.Ndipo Iye adachepetsa mphamvu ya chinthu chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amaganiza mofatsa
١٤.Auze iwo amene amakhulupirira kuti akhululukire iwo amene sakhulupirira m’masiku a Mulungu kuti Iye akhoza kulipira anthu chimene amachita
١٥.Aliyense amene amachita zabwino amachitira mzimu wake ndipo aliyense amene amachita zoipa adzilakwira yekha. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu
١٦.Ndithudi Ife tidawapatsa ana a Israyeli Buku ndi luntha lozindikira mawu a Mulungu ndi Utumwi ndipo tidawapatsa zinthu zokoma ndipo tidawakonda iwo kuposa mitundu ina yonse
١٧.Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zooneka za chipembedzo. Ndipo iwo adayamba mipatuko pamene nzeru zidaperekedwa kwa iwo chifukwa cha njiru pakati pawo. Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku lachiweruzo pa nkhani zimene anali kutsutsana
١٨.Ndipo iwe takuika pa njira yoyenera. Motero tsatira yoyenerayo ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene sadziwa chilichonse
١٩.Ndithudi iwo sangakuthandize chilichonse ku mkwiyo wa Mulungu. Ndi anthu oipa okha okha omwe amakhala ngati atetezi a wina ndi mnzake koma Mulungu ndi Mtetezi wa iwo amene amalewa zoipa
٢٠.Uwu ndi umboni womveka kwa anthu ndi langizo ndi chisomo kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro chokhazikika
٢١.Kodi anthu amene amachita zoipa amaganiza kuti Ife tidzawasamala monga mmene tidzasamalire anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino zofanana ndi moyo wawo ndiponso imfa yawo? Iwo amaweruza molakwa
٢٢.Ndipo Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi kuti mzimu uliwonse ukhoza kupeza dipo lake molingana ndi zimene udachita ndipo palibe amene adzaponderezedwa
٢٣.Kodi wamuona iye amene amasandutsa zilakolako zake kukhala mulungu wake? Mulungu wamusocheretsa iye ndipo wakhazikitsa chophimba m’makutu mwake ndi mu mtima mwake. Ndipo waika chophimba m’maso mwake? Kodi ndani amene akhoza kumutsogolera iye kupatula Mulungu? Kodi tsopano simudzakumbukira
٢٤.Ndipo iwo amati, “Kulibe china chilichonse kupatula moyo wathu wa pa dziko lapansi. Ife timakhala ndi moyo ndipo timafa ndipo palibe chimene chimationonga ife koma nthawi yokha ndiyo.” Ndipo iwo sadziwa chilichonse cha izo koma amangonena zongoganiza
٢٥.Ndipo pamene chivumbulutso chathu chomveka chimanenedwa kwa iwo, mtsutso wawo siukhala wina koma kuti, “Bweretsa makolo athu akale ngati zimene ukunena ndi zoonadi.”
٢٦.Nena: “Mulungu amakupatsani inu moyo, amakuphani ndipo Iye adzakusonkhanitsani pa tsiku la kuuka kwa akufa limene lilibe chikayiko. Koma ambiri sadziwa zimenezi.”
٢٧.Mulungu! Wake ndi ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo patsiku limene ola lidzadza, onse amene amanenazinthuzabodzaadzatayachilichonse
٢٨.Ndipoiwe udzaona mtundu uliwonse utagwada pansi ndipo mtundu uliwonse udzaitanidwa monga mmene zidalembedwera. Lero mudzalipidwa molingana ndi zimene mudachita
٣٠.Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ambuye wawo adzawalowetsa m’chisomo chake. Kumeneku ndiko kupambana kwenikweni
٣١.Koma iwo amene sadakhulupirire adzauzidwa kuti, “Kodi chivumbulutso changa sichidalakatulidwe kwa inu? Koma inu munali onyada ndipo munali anthu ochita zoipa.”
٣٢.Ndipo pamene zidanenedwa kuti, “Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo palibe zokayikitsa za kudza kwa Ola”, inu mudati, “Ife sitidziwa kuti Ola ndi chiyani ndipo ife sitiliganiza kupatula kuti ndi maganizo opanda pake ndipo ife sitilikhulupirira ayi.”
٣٣.Ndipozoipazonsezimeneadachitazidaonekerapoyera kwa iwo ndipo zonse zimene anali kunyoza zidzawapeza
٣٤.Ndipo kudzanenedwa kuti, “Lero takuiwalani inu monga momwe inu mudaiwalira za tsiku lanuli. Ndipo malo anu okhala ndi ku Moto ndipo kumeneko sikudzakhala wina wokuthandizani.”
٣٥.“Ichi ndi chifukwa chakuti mudatenga chivumbulutso cha Mulungu ngati chinthu choseweretsa ndipo moyo wa padziko lino lapansi udakunyengani inu.” Motero patsiku limeneli, iwo sadzachotsedwa ndipo sadzaloledwa kukonza zolakwa zawo
٣٦.Motero kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa Kumwamba ndi Ambuye wa padziko lapansi ndi Ambuye wa zolengedwa zonse