٢.Kodi anthu amaganiza kuti adzasiyidwa okha osayesedwa chifukwa anena kuti, “Ife ndife okhulupirira?”
٣.Ndipo ndithudi Ife tidawayesa anthu amene adalipo iwo asanadze. Ndithudi Mulungu adzawazindikira iwo amene ndi olungama, ndipo ndithudi, adzawazindikira iwo amene ndi abodza
٥.Aliyense amene amakhulupirira kuti adzakumana ndi Mulungu nthawi imene Mulungu adakhazikitsa, ndithudi, idzabwera ndipo Iye ndi wakumva ndi wodziwa
٦.Ndipo aliyense amene adzipereka kwathunthu, akudzipereka podzithandiza iye mwini. Ndithudi Mulungu ndi woima payekha ndipo Iye safuna thandizo lochokera kwa zolengedwa zake
٧.Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ife tidzawakhululukira machimo awo ndikuwapatsa malipiro ofanana ndi ntchito zawo zabwino
٨.Ndipo Ife tidamulamula munthu kuonetsa ubwino kwa makolo ake koma ngati iwo akuuza kuti uzindiphatikiza Ine ndi ena ake amene iwe siuwazindikira, usawamvere ayi. Kwa Ine ndiko mudzabwerera ndipo ndidzakuuzani zimene munali kuchita
٩.Ndipo iwo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, ndithudi, Ife tidzawaika m’gulu la anthu angwiro
١٠.Ndipo pakati pa anthu pali iye amene amati, “Ife timakhulupirira mwa Mulungu.” Koma akangoona mavuto chifukwa chodzipereka kwa Mulungu, amaganiza kuti kuponderezedwa kwawo ndi anthu ndi mkwiyo wochokera kwa Mulungu! Ndipo ngati thandizo lidza kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako, ndithudi, iwo adzati, “Ife tidali kumbali yako.” Kodi mukuganiza kuti Mulungu sadziwa zonse zimene zili m’mitima mwawo pakati pa zolengedwa zake zonse
١٢.Ndipo anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Tsatirani njira yathu ndipo ife tidzavomera chilango chifukwa cha kuchimwa kwanu. Iwo sadzavomera chilango china chilichonse m’malo mwawo. Ndithudi iwo ndi abodza
١٣.Iwo adzanyamula mtolo wawo pamodzi ndi mitolo ina ndi yawo. Ndipo patsiku lachiweruzo iwo adzafunsidwa kufotokoza mabodza awo
١٤.Ndipo ndithudi tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo adakhala pakati pawo zaka chikwi chimodzi kuchotsapo zaka makumi asanu. Ndipo chigumula chidawapeza ali pa uchimo
١٥.Kotero tidamupulumutsa iye pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo ndipo tidachipanga icho kukhala phunziro kwa anthu a mitundu yonse
١٦.Ndipo Ife tidamupulumutsa Abrahamu pamene adati kwa anthu ake, “Pembedzani Mulungu ndipo muzimuopa Iye. Chimenecho chidzakhala chinthu chabwino kwa inu ngati mukadazindikira.”
١٧.Chifukwa inu mumapembedza mafano oonjezera pa Mulungu ndipo inu mumapeka bodza. Zinthu zimene mumapembedza zoonjezera pa Mulungu zilibemphamvuzokupatsanizofunazanu.Koteropemphani zofuna zanu kwa Mulungu ndipo muzimuthokoza Iye. Kwa Iye ndiko kumene mudzabwerera
١٨.Ndipo ngati inu mukana uthenga dziwani kuti nawonso amene adalipo inu musanadze adachita chimodzimodzi. Ndipo udindo wa Mtumwi ndi kulalikira pagulu momveka
١٩.Iwo sakuona mmene Mulungu amayambitsira chilengedwe ndiponso mmene amachibwerezanso. Ndithudi zimenezo ndi za pafupi kwa Mulungu
٢٠.Nena, “Yendani paliponse pa dziko lapansi ndipo muone mmene Mulungu adayambitsira chilengedwe. Kotero Mulungu adzalenga chilengedwe chinanso. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”
٢١.Iye amalanga aliyense amene wamufuna ndiponso amaonetsa chifundo chake kwa aliyense amene wamufuna. Ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera
٢٢.Kaya ndi pa dziko lapansi kapena kumwamba, kulibe kumene inu mungathawire. Ndipo inu mulibe wina kupatula Mulungu amene angakutetezeni kapena kukuthandizani
٢٣.onse amene amakana zizindikiro za Mulungu ndiponso zokumana naye m’moyo umene uli nkudza ndiwo amene amakayika za chifundo changa. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa kwambiri
٢٤.Yankho la anthu a Abrahamu lidali lamwano ndipo adati, “Mumuphe kapena mumutenthe.” Koma Mulungu adamupulumutsa iye ku moto. Ndithudi mu zimenezi muli phunziro kwa anthu okhulupirira
٢٥.Ndipo iye adati, “Inu mwasankha kupembedza mafano kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa chokweza mgwirizano wa pakati panu m’moyo uno. Koma pa tsiku lachiweruzo inu mudzakanana wina ndi mnzake. Ndipo malo anu akakhala ku moto ndipo inu simudzakhala ndi wina wokuthandizani.”
٢٦.Koma Loti adamukhulupirira iye. Iye adati, “Ndidzachoka pa nyumba yanga chifukwa cha Ambuye wanga chifukwa Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wanzeru.”
٢٧.Ndipo tidamupatsa Abrahamu, Isake ndiYakobo ndipo tidakhazikitsa pakati pa ana ake utumiki ndi chivumbulutso. Ndipo Ife tidamupatsa mphotho yake m’moyo uno ndipo iye adzakhala m’moyo umene uli nkudza, pagulu la anthu olungama
٢٨.Ndipo tidatumiza Loti, kotero iye adati kwa anthu ake, “Inu muli kuchita zinthu zonyansa zimene sizidachitikeponso ndi mtundu wa anthu kuyambira kalekale.”
٢٩.“Kodi inu mumakaputa anthu a aamuna ndi kuchita chifwamba m’misewu ndiponso mumaphunzitsa zoipa ngakhale m’magulu anu?” Iwo sadayankhe china chilichonse kupatula kuti iwo adati, “Bweretsa pa ife chilango cha Mulungu ngati iwe ukunena zoona.”
٣١.Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Abrahamu, ndi nkhani ya bwino, iwo adati, “Ndithudi ife tidzaononga anthu a mu mzinda uno chifukwa anthu ake ndi osalungama.”
٣٢.Iye adati, “Ndithudi mu mzindamo muli Loti.” Iwo adati, “Ife tikudziwa amene ali m’menemo. Ndithudi ife tidzamupulumutsa iye ndi omutsatira ake onse kupatula mkazi wake. Iye adzakhala m’gulu la anthu otsalira.”
٣٣.Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Loti, iye anada nkhawa pa zimene zingawachitikire iwo ndipo iye adaoneka wopanda mphamvu yowateteza iwo. Ndipo iwo adati, “Usaope kapena kuda nkhawa. Ndithudi ife tidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi okutsatira ako kupatula mkazi wako. Iye adzakhala m’gulu la anthu otsalira.”
٣٤.Ndithudi Ife tidzatsitsa chilango kuchokera kumwamba, kuti chilange anthu a mzinda uno chifukwa cha machimo awo
٣٦.Ndipo kwa anthu a ku Midiyani tidatumiza m’bale wawo Shaibu ndipo iye adati, “oh anthu anga! Tumikirani Mulungu ndipo opani tsiku limene lili nkudza ndipo musayambitse chisokonezo m’dziko pochita zinthu zoipa.”
٣٧.Koma iwo adamukana iye, kotero chivomezi chachikulu chidadza pa iwo ndipo mitembo yawo idali lambilambi m’nyumba zawo
٣٨.Ndi Aad ndi Thamoud. Chitsimikizo chake chili m’mabanja a m’mizindayi. Satana adawapangitsa kuganiza kuti ntchito zawo zoipa zidali zabwino ndipo iye adawabweza ku njira yoyenera ngakhale kuti iwo adali anthu anzeru ndi aluntha
٣٩.Ndipo Ife tidaononga Karuni, Farawo ndi Hamani. Ndithudi Mose adadza kwa iwo ndi chiphunzitso chabwino koma iwo anali kukhala mwamwano m’dziko ngakhale kuti iwo sakadatha kutigonjetsa Ife
٤٠.Kotero tidalanga aliyense chifukwa cha machimo ake. Pakati pa iwo padali iwo amene tidawatumizira mvula yamkuntho, ndipo pakati pawo padali iwo amene adavutika ndi mphenzi, ndipo pakati pawo padalinso iwo amene adamezedwa ndi nthaka ndipo padalinso iwo amene tidawamiza ndipo Mulungu sadalakwe ayi koma iwo ndiwo amene adalakwira mizimu yawo
٤١.Fanizo la iwo amene amasankha owateteza kuonjezera pa Mulungu ndi Kangaude amene amamanga nyumba yake yaulusi. Ndipo ndithudi iwo akadayenera kudziwa kuti nyumba ya Kangaude ndi imodzi mwa nyumba zosalimba
٤٢.Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene iwo amapembedza kuonjezera pa Iye ndipo Iye ndi wamphamvu ndi wanzeru
٤٣.Ndipo zitsanzozi tili kuziulula chifukwa cha anthu koma palibe amene amazizindikira koma ophunzira okha
٤٤.Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi. Ndithudi muli phunziro mu zimenezi kwa anthu okhulupirira
٤٥.Lakatula zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera m’Bukundipopitirizakupemphera. Ndithudimapemphero amateteza munthu ku machimo ndi zinthu zoipa. Ndithudi kukumbukira Mulungu ndi chinthu chachikulu ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
٤٦.Ndipo musatsutsane ndi anthu okhulupirira za m’Buku pokhapokha kutakhala koyenera kutero, kupatula okhawo amene amachita zoipa. Nena, “Ife timakhulupirira mu izo zimene zavumbulutsidwa kwa ife ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa inu ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi mmodzi ndipo ife tadzipereka kwa Iye.”
٤٧.Ndipokotero Ifetavumbulutsa Bukulolemekezekakwa iwe. Kotero onse amene tawapatsa Buku amakhulupirira mwa ilo ndipo palibe amene amakana chivumbulutso chathu kupatula anthu osalungama
٤٨.Ndipo iwe siudalakatule za m’Buku lina ili lisanadze. Ndipo iwe siudalembe Buku lina lililonse ndi manja ako. Zikadatero, ndithudi, anthu oyankhula zachabechabe akadakayika
٤٩.Iyayi! Izi ndi ziphunzitso zomveka zimene zili m’mitima ya iwo amene adapatsidwa nzeru ndipo palibe amene amakana chiphunzitso chathu kupatula wosalungama
٥٠.Iwo amati, “Bwanji Ambuye wake sadamupatse zizindikiro?” Nena, ” Zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo ine ndine mchenjezi chabe.”
٥١.Kodi sizidakwanire kuti tavumbulutsa Buku lolemekezeka kwa iwe limene lili kuwerengedwa kwa iwo? Ndithudi m’Bukuli muli chifundo ndi chikumbutso kwa anthu okhulupirira
٥٢.Nena, “Mulungu ndi mboni yokwana pakati pa ine ndi inu. Iye amadziwa chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi.” Ndipo iwo amene amakhulupirira zabodza, ndiponso sakhulupirira mwa Mulungu, amenewa, ndi anthu olephera
٥٣.Iwo amakukakamiza kuti ubweretse chilango msanga. Ndipo zikadakhala kuti nthawi yake siidakhazikitsidwe kale, ndithudi, chilango chikadakhala chitadza kale pa iwo. Ndithudi icho chidzadza pa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sali kuchiganizira
٥٥.Patsiku limene chilango chidzadza pa iwo kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi mawu adzati, “Lawani inu zipatso za ntchito zanu.”
٥٦.oh inu akapolo anga amene mwakhulupirira! Ndithudi dziko langa lili ndi malo ambiri. Kotero ndipembedzeni Ine ndekha
٥٨.Ndipoiwoameneamakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, otere tidzawapatsa malo kumwamba amene pansi pake pamayenda mitsinje kuti akhale m’menemo mpaka kale kale. Eti kukoma mphotho ya iwo amene amachita zabwino
٦٠.Kodi zilipo zolengedwa zingati zimene sizisunga chakudya chawo? Ndi Mulungu amene amazidyetsa izo pamodzi ndi inu nomwe. Ndipo Iye ndi wakumva ndi wodziwa
٦١.Ndithudi ngati iwe utawafunsa kuti kodi ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso amene adalamula dzuwa ndi mwezi kumvera malamulo ake? Ndithudi iwo adzayankha kuti ndi Mulungu. Nanga ndi chifukwa chiyani iwo amakana choonadi
٦٢.Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndipo amamana aliyense amene Iye wamufuna. Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
٦٣.Ngati iwe ungawafunse kuti kodi ndani amene amagwetsa mvula ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali ya kufa? Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Ndi Mulungu.” Nena “Kuyamikidwa konse kukhale kwa Iye.” Iyayi, ambiri a iwo sazindikira
٦٤.Ndipo moyo wa padziko lapansi siuli kanthu koma masewera ndi kongotayira nthawi. Ukakhala moyo umene uli nkudza, umenewo ndiwo weniweni, iwo akadadziwa
٦٥.Kotero iwo akamakwera zombo amapempha kwa Mulungu modzipereka ndi modzichepetsa. Koma Iye akawafikitsa pa mtunda mwaubwino, Ah! iwo amamufanizira Iye ndi zina zake
٦٦.Kotero iwo amaonetsa kusathokoza pa zimene tawapatsa kuti akhoza kusangalala; ndipo iwo adzazindikira posachedwapa
٦٧.Kodi iwo saona kuti tateteza malo odalitsika pamene anthu ena ali kutengedwa mwankhanza pa malo owazungulira? Kodi iwo adzakhala ali kukhulupirirabe zabodza ndi kukana ubwino wa Mulungu
٦٨.Kodi woipitsitsa ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene amati choonadi ndi chabodza pamene auzidwa za icho? Kodi Gahena siidzakhala malo okhalamo anthu onse osakhulupirira
٦٩.Akakhala iwo amene amalimbikira kugwira ntchito yathu,ndithudi, Ife tidzawatsogolera ku njira zathu. Ndithudi Mulungu amakhala ndi iwo amene amachita zabwino