٤.Ngati Ife tifuna, tikhoza kuwavumbulutsira chizindikiro chochokera kumwamba chimene makosi awo adzakhota modzichepetsa
٦.Ndithudi iwo amakana mawu a Mulungu koma nkhani zidzadza kwa iwo zokhudza zinthu zimene iwo amazichita chipongwe
١٥.Mulungu adati, “Nkosatheka kutero! Kotero pitani nonse awiri ndi zizindikiro zathu. Ife tidzakhala ndi inu ndipo tidzamva.”
١٦.Ndipo mukakafika kwa Farawo mukamuuze kuti, “Ife ndife Atumwi ochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”
١٨.(Farawo) adati, “Kodi ife sitidakurere iwe pamene udali wamng’ono? Ndipo iwe unakhala pakati pathu zaka zambiri.”
٢٠.(Mose) adati, “Ine ndidachita chimenecho popeza nthawi imeneyo ndidali wosadziwa china chilichonse.”
٢١.“Motero ine ndidathawa inu nonse pa nthawi imene ndidakuopani koma tsopano Ambuye wanga wandipatsa luntha ndiponso wandipanga ine kukhala mmodzi mwa Atumwi ake.”
٢٢.“Ndipo uwu ndi mwayi umene ubwino wake iwe uli kundinyogodola. Iwe wasandutsa ana a Israyeli kukhala akapolo ako.”
٢٤.(Mose) adati, “Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo ngati inu mufuna kukhulupirira.”
٢٨.(Mose) adati, “Iye ndi Ambuye wa kum’mawa ndi kumadzulo ndi zonse zimene zikhala kumeneko ngati muli ozindikira.”
٢٩.(Farawo) adayankha kuti, “Ngati iwe utumikira mulungu wina kupatula ine, ndithudi ndikupanga kukhala mmodzi wa anthu okhala ku ndende.”
٣٠.(Mose) adafunsa kuti, “Kodi zingakhale choncho ngakhale nditakulangiza chizindikiro choonekeratu? “
٣٥.“Iyeyu afuna kukuchotsani m’dziko lanu ndi matsenga ake. Kodi ulangizi wanu ndi wotani ndipo ukupereka langizo lanji?”
٣٦.Iwo adati, “Muyambe mwawasunga iye pamodzi ndi m’bale wake kwa kanthawi kochepa. Tumizani mithenga ku mizinda yanu
٤١.Ndipo pamene anthu onse amatsenga adadza kwa Farawo, iwo adati kwa Farawo, “Kodi mudzatilipira ngati titapambana?”
٤٤.Ndipo iwo adaponya zingwe ndi ndodo zawo ndipo adati: “Mwa mphamvu ya Farawo, ndithudi, ife tipambana.”
٤٩.Farawo adati, “Kodi inu mwakhulupirira mwa iye pamene ine sindinakupatseni chilolezo? Ndithudi iye ndi mtsogoleri wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi posachedwapa mudzazindikira. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu moisiyanitsa. Ndidzakudulani dzanja lamanja ndi mwendo wamanzere ndiponso ndidzakupachikani pa mtanda.”
٥١.“Ndithudi Ife tili ndi chiyembekezo kuti Ambuye wathu adzatikhululukira machimo athu popeza ndife oyamba kukhulupirira.”
٥٢.Ndipo tidamulamula Mose kuti, “Nyamuka nthawi ya usiku ndi akapolo anga chifukwa, ndithudi, inu mulondoledwa ndi gulu la adani anu.”
٦٣.Ndipo tidalamulira Mose kuti, “Menya madzi a m’nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo nyanja idagawanika pakati, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu
٧٠.Pamenepo iye adanena kwa abambo ake ndiponso kwa anthu ake kuti, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?”
١٠٩.“Ine sindikupemphani malipiro ena alionse chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire ine kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
١١٨.Motero weruzani mwachilungamo pakati pa ine ndi iwo. Ndipulumutseni ine pamodzi ndi anthu okhulupirira amene ali ndi ine
١٢٧.“Pa ntchito iyi, ine sindipempha malipiro kuchokera kwa inu chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
١٣٩.Iwo adamukana iye ndipo Ife tidawaononga onse. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro koma ambiri sakhulupirira ayi
١٤٥.“Pa ntchito iyi ine sindili kukupemphani malipiro. Palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
١٥٥.Iye adati, “Iyi ndi ngamira yaikazi. Iyo idzamwa madzi patsiku lake ndipo inu mudzamwa patsiku lanu lokhazikitsidwa.”
١٥٨.Chilango chidawapeza iwo. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro koma ambiri a iwo sakhulupirira
١٦٤.“Ine sindili kupempha kuti mundilipire chifukwa cha ichi ayi chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
١٨٠.“Ine sindikupemphani malipiro chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
١٨٩.Iwo adamukana iye kotero chilango cha thambo ndi moto chidawaononga. Ichi chidali chilango cha tsiku loopsa
٢١٣.Musapembedze milungu ina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mukatero mudzakhala m’gulu limene lidzalangidwa
٢٢٧.Kupatula okhawo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndi kumakumbukira Mulungu kwambiri ndi kudziteteza pambuyo pa kuponderezedwa. Ndipo iwo amene amachita zoipa adzadziwa chimene chidzawagadabuza