علق
الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja
1.
Werenga! M’dzina la Ambuye wako amene analenga
2.
Yemwe adalenga munthu kuchokera ku kadontho kamagazi oundana
3.
werenga! Ndipo Ambuye wako ndiye wopereka mowoolowa manja
4.
Amene anaphunzitsa ndi cholembera
5.
Anaphunzitsa munthu chimene sanali kuchidziwa
6.
Iyayi! Ndithudi, munthu amalakwa mopyola muyeso
7.
Chifukwa amaganiza kuti iye ndi oima payekha
8.
Ndithudi! Nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu
9.
Kodi mwamuona munthu amene amaletsa
10.
Kapolo pamene akupemphera
11.
Kodi mwamuona ngati iye alikutsatira chilangizo chabwino
12.
Kapena kulamulira machitidwe abwino
13.
Ndiuze ngati iye akana choonadi ndipo salabadira
14.
Kodi iye sadziwa kuti Mulungu amaona zinthu zonse
15.
Iyayi! Ngati iye sasiya, Ife tidzamududuluza pogwira tsitsi la pa mphumi pake
16.
Mphumi yabodza ndi yochimwa
17.
Ndipo mulekeni iye aitane anzake oti amuthandize
18.
Ife tidzaitana osunga Gahena
19.
Iyayi! Usamumvere iye. Gunditsa mphumi yako pansi ndipo idza pafupi ndi Mulungu
پچھلی سورہ
اگلی سورہ