الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.Iwo akukufunsa iwe za katundu amene mumapeza mukamenya nkhondo. Nena: “Mwini wake wa katundu uyu ndi Mulungu ndi Mtumwi. Motero muopeni Mulungu ndipo yanjanani pakati panu ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ngati inu ndinu okhulupirira.”
42.Ndi pamene inu mudali tsidya lino la dambo ndi pamene anthu osakhulupirira adali tsidya ilo ndi magareta mmunsi mwanu. Ngakhale inu mukadagwirizana za malo okumana, inu mukadalephera kukwaniritsa chipanganocho koma Mulungu adafunitsitsa kuti akwaniritse zonse zimene adalamulira kuti aliyense amene adalembedwa kuti adzaonongeka, aonongeke pamene atalandira malangizo ooneka ndipo kuti iwo amene adalembedwa kuti asafe akhale ndi moyo atalandira malangizo ooneka. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
72.Ndithudi iwo amene adakhulupirira ndi kusamuka ndipoanapilirandikumenyankhondondichumachawondi iwoenim’njiraya Mulungundipondiiwoameneadawasunga ndi kuwathandiza, amenewa adzakhala a bwenzi a wina ndi mnzake. Iwo amene akhulupirira koma sadasamuke mwa njira iliyonse iwe ulibe udindo pa iwo pokhapokha ngati iwo asamuka. Koma ngati iwo afuna chithandizo cha chipembedzo ndi udindo wako kuwathandiza kupatula anthu amene ali ndi pangano logwirizana pakati pa inu ndi iwo ndipo Mulungu amaona ntchito zanu zonse