7.Chimene Mulungu adachilamulira kuti chikunthe pa iwo usiku usanu ndi uwiri ndi usana usanu ndi utatu mosalekeza. Moti iwe ukadawaona anthu atagonagona ukadayesa kuti ndi mitengo ya migwalangwa yakugwa
9.Ndipo Farao ndi anthu amene adalipo iye asadabadwe, ndi a mizinda imene idaonongeka anali kuchita zoipa
10.Ndipo iwo sanamvere Mtumwi wochokera kwa Ambuye wawo ndipo Iye adawalanga ndi chilango chowawa zedi
17.Ndipo Angelo adzaima mbali zonse ndipo angelo asanu ndi atatu pa tsikuli adzanyamula Mpando wa Chifumu wa Ambuye wako
19.Ndipo yense amene adzapatsidwa Buku lake kudzanja lamanja adzati: “Ah taonani! Werengani Buku langa!”
24.Idyani ndipo imwani mmene mufunire chifukwa cha ntchito zanu zabwino zimene mudatumiza patsogolo panu m’masiku apitawo
25.Koma iye amene adzapatsidwe buku lake m’dzanja lamanzere, adzati: “Kukadakhala bwino ngati Buku langa likadakhala losaperekedwa kwa ine.”