الحاج یوسف محمد کنیمولا · chiCheŵa, chinyanja

1.oh inu anthu amene mwakhulupirira! Musasandutse adani anga ndi adani anu kukhala abwenzi anu powaonetsa chikondi chanu pamene iwo akana choonadi chimene chadza kwa inu ndipo amupirikitsa Mtumwi pamodzi ndi inu nomwe kuchokera ku nyumba zanu, chifukwa chakuti inu mumakhulupirira mwa Mulungu Ambuye wanu. Ngati inu mwadza ndi cholinga chogwira ntchito m’njira yanga ndi kufunafuna chisangalalo changa(musachite nawo ubwenzi). Ndipo ngati inu mumaonetsa chikondi kwa iwo mwamseri, ndithudi, mukatero mwasochera. Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita mseri
4.Muli chitsanzo chabwino kwa inu mwa Abrahamu ndi mwa iwo amene adali naye pamene iwo ananena kwa anthu awo kuti: “Ife sitili m’gulu lanu ndipo sitipembedza zimene inu mumapembedza pozifanizira ndi Mulungu. Ife takukanani ndipo pabuka pakati pa ife ndi inu udani ndi chidani chosatha kupatula ngati inu mukhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Iye yekha.” Kupatula zonena za Abrahamu kwa Abambo ake kuti: “Ine ndidzapempha chikhululukiro chanu chifukwa ine ndilibe mphamvu pa chilichonse cha inu kuchokera kwa Mulungu. Ambuye wathu, mwa Inu ife takhulupirira ndi kwa Inu ndiko timapempha chikhululukiro, ndipo kwa Inu ndiko kumene tonse tidzabwerera pomaliza.”
10.Oh inu anthu okhulupirira! Pamene akazi okhulupirira adza kwa inu ngati othawa mavuto, afufuzeni bwinobwino. Mulungu yekha ndiye amene adziwa bwino bwino chikhulupiriro chawo. Ngati inu mukhutitsidwa kuti ndi okhulupirira m’choonadi, musawabwezere kwa anthu osakhulupirira chifukwa iwo saloledwa kukwatiwa ndi anthu osakhulupirira monga momwe amuna osakhulupirira saloledwa kukwatira akazi okhulupirira. Koma abwezereni anthu osakhulupirira ziwongo zimene apereka. Ndipo sikulakwa ngati inu muwakwatira akazi okhulupirirawa ngati mwapereka chiwongo. Musapitilize ukwati wanu ndi akazi wosakhulupirira. Itanitsani zimene mwaononga ngati chiwongo cha ukwati ndipo aloleni osakhulupirira kuti nawonso aitanitse zimene aononga pa akazi okhulupirira amene adza kwa inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Iye amaweruza mwachilungamo pakati panu. Mulungu ndi wa nzeru ndi luntha