23.Awa ndi mayina chabe amene inu mwapeka, inu ndi atate anu, amene Mulungu sadakulamuleni ndi pang’ono pomwe. Iwo amangotsatira nkhani zakumva chabe zimene mitima yawo imafuna pamene, ndithudi, kwadza kale kwa iwo ulangizi wochokera kwa Ambuye wawo
26.Ndipo kuli angelo ambiri amene ali kumwamba amene kukhala pakati kwawo sikudzathandiza chilichonse kupatula pokhapo pamene Mulungu apereka chilolezo kwa amene Iye wamufuna ndi kukondweretsedwa naye
28.Pamene iwo sadziwa chilichonse cha izo. Iwo satsatira china chilichonse koma nkhani zabodza ndipo, ndithudi, nkhani zabodza si mlowam’malo wa choonadi
29.Motero mupewe wina aliyense amene salabadira chikumbutso chathu ndipo safuna china chilichonse koma moyo wa padziko lino lapansi
30.Uko ndiko kuchuluka kwa nzeru zawo. Ndithudi Ambuye wako ndiye amadziwa bwino onse amene amasochera ku njira yoyenera ndipo amadziwa kwambiri iye amene amatsata njira yoyenera
31.Ndipo Mulungu ndiye mwini wake wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo akhoza kulanga onse amene amachita zoipa molingana ndi ntchito zawo ndiponso kuti akhoza kulipira onse amene amachita zabwino ndi mphotho yabwino kwambiri
32.Iwo amene amapewa machimo a akuluakulu ndi chigololo kupatula machimo a ang’onoang’ono, ndithudi, Ambuye wako ndi Mwini chikhululukiro. Iye amakudziwani bwino pamene amakulengani kuchokera ku dothi ndi pamene mukutidwa m’mimba mwa amayi anu. Motero musadziyeretse nokha. Al Najm 567 Iye amadziwa bwino kwambiri aliyense amene amalewa zoipa