23.Ndiye, pali Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chimenechi ndi cholinga ndi choonadi chomwe inu mumayankhula
25.Pamene iwo adadza kwa iye, iwo adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Inu ndinu alendo kwa ine.”
28.Motero iye adayamba kuchita mantha mu mtima mwake. Ndipo iwo adati, “Usaope.” Ndipo iwo adamuuza nkhani yabwino yakubadwa kwa mwana wamwamuna yemwe adzakhala wanzeru kwambiri
29.Ndipo mkazi wake adadza modzichepetsa ndipo adamenya pa mphumi pake nati, “Nkhalamba yaikazi yosaberekapo!”
30.Iwo adati, “Ngakhale ndi choncho, Ambuye wako wayankhula. Iye ndi wodzala ndi luntha ndiponso nzeru.”
39.Koma Farawo adakana pamodzi ndi mafumu ake nati, “Ndiwe munthu wamatsenga kapena munthu wa misala.”
40.Motero tidamugwira pamodzi ndi gulu la asirikali ake ndi kuwamiza onse m’nyanja pamene iye ndiye adali wolakwa
42.Imene sidasiye chilichonse chimene idalimbana nacho kupatula kuchiononga ndi kuchisandutsa phulusa
47.Ife tidakonza kumwamba mwamphamvu ndiponso mwaluso. Ndipo, ndithudi, ndife amene timapanga kukula kwa mlengalenga
51.Ndipo musapange fano kukhala lopembedzedwa pamodzi ndi Mulungu. Ndithudi ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye
52.Chimodzimodzi palibe Mtumwi amene adadza kwa anthu amene sadamunenere mawu ofanana monga akuti: “Wamatsenga kapena munthu wopenga!”
53.Kodi uwu ndi mwambo umene akhala ali kusiyirana wina ndi mnzake? Iyayi, iwo ndi anthu amene ali kuswa malamulo mopyola muyeso
58.Ndithudi ndi Mulungu yekha amene amapereka chakudya chonse, Mwini mphamvu zonse ndi wolimba kwambiri
59.Ndithudi anthu onse olakwa adzalandira gawo longa limene anzawo olakwa akale adalandira, kotero asandifunse Ine kuchita mofulumira